Pitani ku nkhani yake

Kodi Ndingatani Kuti Ndizigwirizana Ndi Aphunzitsi Anga?

Kodi Ndingatani Kuti Ndizigwirizana Ndi Aphunzitsi Anga?

Ganizirani nkhaniyi mozama

Taganizirani za Rachel. Rachel ankakhoza bwino kwambiri mayeso. Koma zinthu zinasintha atafika chaka cha 7 ali pasukulupo. Iye anati: “Aphunzitsi anga ankapangitsa kuti ndisamakhoze m’kalasi.” Kodi vuto linagona pati? Aphunzitsiwo sanam’bisire Rachel ndi mayi ake omwe, koma anasonyeza moonekeratu kuti amadana ndi chipembedzo chimene mtsikanayo ndi mayi ake ali.

Aphunzitsi ali ngati miyala imene mungaponde powoloka kuchoka ku umbuli n’kukhala munthu wophunzira. Komabe inuyo mukufunika kuyenda

N’chiyani chinachitika? Rachel anati: “Nthawi zonse zinkachita kuonekera kuti aphunzitsiwo akundilepheretsa dala mayeso chifukwa chodana ndi chipembedzo changa. Ndipo zimenezi zikachitika, mayi anga ankabwera kudzakambirana ndi aphunzitsiwo. Patapita nthawi, aphunzitsiwo anasiya khalidwe lawolo.”

Ngati inuyo mukukumana ndi vuto ngati limeneli, limbani mtima n’kukauza makolo anu. N’zosakayikitsa kuti makolo anuwo adzakhala okonzeka kukalankhula ndi aphunzitsiwo kapena akuluakulu ena oyendetsa sukuluyo n’cholinga choti vutolo lithe.

Komabe kuchita zimenezi sikuti nthawi zonse kumathetsa mavuto onse. Nthawi zina mungafunike kungopirira. (Aroma 12:17, 18) Mtsikana wina dzina lake Tanya anati: “Mphunzitsi wathu wina anali wankhanza kwambiri. Nthawi zambiri ankatinyoza, n’kumatinena kuti ndife opusa. Poyamba mphunzitsiyo akatinyoza ndinkalira, koma kenako ndinaona kuti ndisamaganizire kwambiri zimene ankanenazo. Ndinasankha zoti ndizingoganizira kwambiri zimene mphunzitsiyo akuphunzitsa. Zimenezi zinandithandiza kuti ndisamadandaule kwambiri akamatinyoza. Zotsatira zake n’zakuti ndinali m’gulu la ana ochepa kwambiri m’kalasimo amene ankakhoza bwino. Patapita zaka ziwiri, mphunzitsiyo anachotsedwa ntchito.”

Dziwani izi: Ngati aphunzitsi anu ali ovuta kwambiri, phunzirani kupirira. Zimenezi zidzakuthandizani kuti mukhale ndi luso lapadera lomwe lingadzakuthandizeni kupirira m’tsogolo muno mukadzayamba kugwira ntchito ndi abwana ovuta. (1 Petulo 2:18) Mudzaphunziranso kuyamikira mukadzakhala ndi aphunzitsi ena abwino.