Pitani ku nkhani yake

Bwanji Ngati Akundikakamiza Kuti Ndigone Naye?

Bwanji Ngati Akundikakamiza Kuti Ndigone Naye?

Mwina mungaganize kuti, “Kodi ndingololera? Ndikuona kuti palibe vuto lililonse chifukwa anzanga onse akumagonana.”

Ganizirani izi:

Zoona zake: Sikuti anzanu onse amagonana.

N’zoona kuti mungawerenge nkhani zina zosonyeza kuti anthu ambiri amagonana. Mwachitsanzo, zotsatira za kafukufuku wina amene anachitika m’dziko la United States zinasonyeza kuti pa ana asukulu atatu alionse amene akumaliza maphunziro awo a kusekondale, ana awiri amakhala atayamba kale kugonana. Koma zimenezi zikusonyezanso kuti mwana wasukulu mmodzi pa ana atatu alionse amakhala woti sanagonanepo ndi munthu.

Kodi chimachitika n’chiyani kwa achinyamata amene amagonana? Malinga ndi kafukufuku, zikuoneka kuti ambiri mwa achinyamata amenewa amakumana ndi mavuto osiyanasiyana monga otsatirawa.

Kuvutika Maganizo. Achinyamata ambiri amene anachitapo zachiwerewere amanena kuti ananong’oneza bondo pambuyo pake.

Kugonana ndi munthu amene simunakwatirane naye kuli ngati kutenga chithunzi chokongola kwambiri n’kuchisandutsa chopondapo

Kukayikirana. Achinyamata akachita chiwerewere, amayamba kudzifunsa kuti, ‘Kodi amene ndagona nayeyu wagona ndi anthu angati?’

Kukhumudwitsidwa. Ngakhale kuti sanganene, atsikana ambiri amafuna mnyamata amene angawateteze, osati kuwadyera masuku pamutu. Ndipo anyamata ambiri akagona ndi mtsikana, sakopeka nayenso ndipo amayamba kumuona ngati wopanda ntchito.

Dziwani izi: Thupi lanu ndi lamtengo wapatali, choncho si nzeru kugonana ndi munthu musanakwatirane. Yesetsani kumvera lamulo la Mulungu lakuti mupewe dama. Mukadzakwatira mudzakhala ndi ufulu wogonana ndi mwamuna kapena mkazi wanu. Ndipo muzidzachita zimenezi mosangalala, popanda kuopa mavuto amene anthu amene amagonana asanakwatirane amakumana nawo.—Miyambo 7:22, 23; 1 Akorinto 7:3.