Tsamba la Mfundo Zokhudza Maofesi Ndiponso Kuona Malo ku United States lakonzedwanso. Panopo tsambali lili ndi mfundo zatsopano zokuthandizani kudziwa zimene mungachite musanapite kukaona malo komanso nthawi imene muyenera kufika kumaofesiwo pokaona malo. Patsambali palinso linki imene mungapangepo dawunilodi pepala losonyeza likulu lathu la dziko lonse ku Warwick.