Pitani ku nkhani yake

OCTOBER 8, 2018
ZATSOPANO

Mabuku Atsopano Komanso Mawebusaiti ndi Mapulogalamu Okonzedwanso

Mabuku Atsopano Komanso Mawebusaiti ndi Mapulogalamu Okonzedwanso

Pa msonkhano wapachaka wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, womwe unachitika pa 6 October, 2018, panatulutsidwa mabuku awiri atsopano. Buku lachingelezi la mutu wakuti Pure Worship of JehovahRestored At Last! lili ndi nkhani zochokera mu ulosi wa Ezekieli, ndipo kabuku kamutu wakuti Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso kakonzedwa kuti kathandize a Mboni za Yehova kuti aziwerenga komanso kuphunzitsa mwaluso kwambiri.

Panopa pa webusaiti ya jw.org komanso pa JW Library, pakupezeka buku lachingelezi la Pure Worship komanso kabuku ka Kuphunzitsa komwe kakupezeka m’ziyankhulo zambiri. M’tsogolomu buku la Pure Worship lidzayamba kutulutsidwa m’ziyankhulo zinanso.

Pamsonkhanowu panalinso chilengezo choti Bungwe Lolamulira lavomereza kuti mawebusaiti athu komanso mapulogalamu ena zikonzedwenso. Webusaiti ya jw.org ikonzedwa kuti izikhalanso ndi zinthu zomwe zimapezeka pa JW Broadcasting ndi pa LAIBULALE YA PA INTANETI ya Watchtower. Kuonjezera pamenepo, pulogalamu ya JW Library ikonzedwa kuti izikhalanso ndi zinthu zomwe zimapezeka pa Watchtower Library komanso zinthu zomwe zimangopezeka pa webusaiti ya jw.org pokha. Webusaiti yatsopano limodzinso ndi pulogalamu yatsopanoyi zizioneka mofanana komanso zikhala zosavuta kugwiritsa ntchito. Mwachitsanzo, pofuna kuthandiza anthu kuti azipeza chakudya chauzimu mwachangu, zinthu zina za pa webusaiti ndi pulogalamu yatsopanoyi zidzakonzedwa m’njira yakuti anthu asamavutike kupeza zomwe akufuna. Ntchito yokonzekera komanso kukonza mmene webusaiti ndiponso pulogalamuyi zizidzaonekera yayambika kale. Muyamba kuona kusinthaku m’miyezi ikubwerayi.