Pitani ku nkhani yake

OCTOBER 9, 2019
ZATSOPANO

Mawebusaiti a JW Broadcasting ndi JW.ORG Aphatikizidwa

Mawebusaiti a JW Broadcasting ndi JW.ORG Aphatikizidwa

Webusaiti ya JW Broadcasting (tv.jw.org) yaphatikizidwa ndi webusaiti ya jw.org.

Gawo lakuti Mabuku lomwe lili pa jw.org lasinthidwa ndipo lizidziwika kuti Laibulale, chifukwa tsopano pagawoli pali mavidiyo ambiri ndi zinthu zongomvetsera zambiri. Mavidiyo onse kuphatikizapo omwe m’mbuyomu anaikidwa pa tv.jw.org pokha tsopano azipezeka pa jw.org pagawo lakuti LAIBULALE > MAVIDIYO.

Sipakhalanso gawo lapadera lakuti TV lomwe linkapezeka pa tv.jw.org. M’malomwake, pagulu lililonse la mavidiyo (tchanelo) tsopano pazikhala mbali yakuti, Onerani Tchaneloyi. Sankhani mbali imeneyi kuti muonere mavidiyo onse omwe ali m’gulu limenelo mosatsatira mndandanda.

Onani gawo la Mavidiyo pa jw.org.