Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lokonzedwanso linatulutsidwa m’chiyankhulo cha Chijeremani pa 2 February, 2019 mumzinda wa Selters ku Germany. Baibulo la Dziko Latsopano lamasuliridwa lathunthu kapena mbali zake zina m’ziyankhulo 179, kuphatikizapo 20 zomwe zakonzanso Mabaibulo awo mogwirizana ndi Baibulo lomwe linatulutsidwa mu 2013.