Pitani ku nkhani yake

MARCH 18, 2019
ZATSOPANO

Baibulo la Dziko Latsopano Linatulutsidwa M’Chishona

Baibulo la Dziko Latsopano Linatulutsidwa M’Chishona

Pa 17 March, 2019, Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lokonzedwanso linatulutsidwa m’chinenero cha Chishona mumzinda wa Harare ku Zimbabwe. Baibulo la Dziko Latsopano lamasuliridwa lathunthu kapena mbali zake zina m’zinenero 179, kuphatikizapo m’zinenero 21 zomwe zakonzanso Mabaibulo awo mogwirizana ndi Baibulo lomwe linatulutsidwa mu 2013.