Pitani ku nkhani yake

OCTOBER 28, 2019
ZATSOPANO

Baibulo la Dziko Latsopano Latulutsidwa M’Chimaya, M’Chitelugu ndi M’Chitsotsilu

Baibulo la Dziko Latsopano Latulutsidwa M’Chimaya, M’Chitelugu ndi M’Chitsotsilu

Pa 25 October 2019, Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika linatulutsidwa m’Chimaya, ku Mérida, Yucatán, m’dziko la Mexico. Tsiku lomwelo, Baibulo la Dziko Latsopano linatulutsidwa m’chinenero cha Chitelugu ku Hyderabad, m’dziko la India komanso m’chinenero cha Chitsotsilu ku Tuxtla Gutiérrez, Chiapas, m’dziko la Mexico. Baibulo la Dziko Latsopano lamasuliridwa lathunthu kapena mbali zake zina m’ziyankhulo 185.