Pitani ku nkhani yake

JULY 22, 2019
ZATSOPANO

Baibulo la Dziko Latsopano Latulutsidwa M’Chiayisilandi ndi M’Chisipanishi

Baibulo la Dziko Latsopano Latulutsidwa M’Chiayisilandi ndi M’Chisipanishi

Pa 19 July, 2019, Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu linatulutsidwa m’Chiayisilandi mumzinda wa Copenhagen ku Denmark. Pa tsiku lomweli, Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lokonzedwanso, linatulutsidwa m’Chisipanishi mumzinda wa Madrid ku Spain. Baibulo la Dziko Latsopano lamasuliridwa lathunthu kapena mbali zake zina m’zinenero 181, kuphatikizapo m’zinenero 25 zomwe zakonzanso Mabaibulo awo mogwirizana ndi Baibulo lomwe linatulutsidwa mu 2013.