HARARE, Zimbabwe—A Mboni za Yehova anayamba kuchita misonkhano yaikulu kuyambira Lachisanu pa 31 July,2015. Misonkhanoyi ili ndi mutu wakuti, “Tsanzirani Yesu.” Misonkhanoyi izichitika kwa masiku atatu ndipo ikhala ikuchitika mpaka cha pakati pa mwezi wa October.

A Geoffrey Jackson, omwe ali m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, akukamba nkhani pamsonkhano wa mayiko wa 2014 womwe unachitikira ku Zimbabwe. Abale awiri omwe akumasulira nkhani m’zinenero za komweko aima pambali pake.

Woyankhula m’malo mwa a Mboni za Yehova ku Zimbabwe, dzina lake John Hunguka, anati: “Tikuyembekezera kuti msonkhano umenewunso ukhala wosaiwalika. Zimene zinachitika chaka chatha pamsonkhano wa mayiko womwe unachitikira ku Harare, zichititsa kuti ambiri abwere pamsonkhanowu. Msonkhano wa 2014 ndi wosaiwalika m’mbiri yonse ya Mboni za Yehova ku Zimbabwe kuno.” Nyuzipepala ina yomwe ndi yotchuka kwambiri ku Zimbabwe inanena kuti ku Zimbabwe sikunachitikeponso “msonkhano waukulu choncho.” Inanenanso kuti msonkhanowu utangochitika mu 2014 “nkhani yonena za a Mboni za Yehova inali m’kamwam’kamwa m’dziko lonselo.”

Anthu oposa 82,000 anapita kubwalo la zamasewera la National Sports Stadium ku Harare pa tsiku lomaliza la msonkhanowu. Woimira ofesi ya Mboni za Yehova ku Zimbabwe, dzina lake John Jubber, anati: “Tinali ndi alendo okwana 3,500 omwe anachokera m’mayiko ena monga Brazil, Germany, United States, Zambia ndi Kenya.”

Chaka chino, a Mboni za Yehova achita misonkhano yokwana 39 ya mutu wakuti “Tsanzirani Yesu.” Misonkhanoyi idzachitikira m’malo osiyanasiyana ndipo wina udzachitikira ku malo a chionetsero cha zamalonda a ku Zimbabwe. Nkhani za pa msonkhanowu zidzakambidwanso mu Chitchainizi (Mandarin), Chitonga (Zimbabwe), Chingelezi, Chindebele (Zimbabwe), Chishona, Chiswahili komanso Chinenero Chamanja cha ku Zimbabwe. Ngati mukufuna kudziwa tsiku komanso malo omwe kudzachitikire misonkhanoyi pitani pawebusaiti yathu ya jw.org.

Yankhulani ndi:

Kuchokera M’mayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Zimbabwe: John Hunguka, tel. +263 4 2910591