NOUMEA, New Caledonia—Kuyambira usiku wa pa 13 March, 2015, mphepo yoopsa inadutsa pazilumba za Vanuatu zomwe zili m’nyanja ya Pacific. Ofesi ya Mboni za Yehova ya ku New Caledonia inanena kuti palibe wa Mboni amene anafa kapena kuvulala pa ngoziyi. Panopa akufufuzabe mmene mphepoyi yawonongera zinthu. Koma pofika pano apeza kuti pachilumba china chotchedwa Efate, nyumba za a Mboni 31 zinawonongeka, ndipo zina 58 zinawonongeka kwambiri. Pachilumba china chotchedwa Tanna, pafupifupi nyumba zonse za a Mboni zinawonongeka kwambiri kapena kugweratu. Mphepoyi inagwetsanso Nyumba za Ufumu zitatu ndipo Nyumba ya Ufumu ina inawonongeka kwambiri mtengo utagwera panyumbayo.

Chifukwa cha zimenezi, panakhazikitsidwa komiti yoti ithandize anthu. Komitiyo inali kulikulu la dziko la Vanuatu lotchedwa Port Vila ndipo inkagawa chakudya, madzi komanso zinthu zina zofunika kwa a Mboni omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi. Komanso inatumiza chakudya ndi zinthu zina kwa a Mboni a pachilumba cha Tanna. A kuofesi ya Mboni za Yehova ya ku Australia ndiponso ku New Caledonia akuyesetsa kuthandiza anthu amene akhudzidwa ndi ngoziyi. Mwachitsanzo akumamanga malo oti anthuwo azikhala mongodikirira, akumakonza nyumba zomwe zinawonongeka komanso akumapereka zinthu zina monga zogonera komanso zovala.

A Jean-Pierre Francine, omwe amayankhula m’malo mwa a Mboni za Yehova ku New Caledonia anati: “Tikuthokoza kwambiri chifukwa cha chithandizo chimene anzathu akutitumizira kuchokera m’mayiko ena. Tikuthokozanso mabungwe a boma amene athandiza anzathu omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi. Ndiye popeza panopa ndege zayambanso kuuluka ku Vanuatu, posachedwapa kubwera woimira ofesi ya Mboni za Yehova wochokera ku New Caledonia komanso a Mboni ena kuti adzalimbikitse ndi kuthandiza a Mboni amene zinthu zawo zinawonongedwa ndi mphepoyi.”

Yankhulani ndi:

Kuchokera ku Mayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

New Caledonia: Jean-Pierre Francine, tel. +687 43 75 00