NEW YORK—A Mboni za Yehova ayamba misonkhano yawo yachigawo ya mutu wakuti “Tsanzirani Yesu,” ndipo msonkhano woyamba udzachitika kuyambira Lachisanu pa May 22, 2015 ku United States. Msonkhanowu, umene udzakhale waulere, udzakhala ukuchitikanso mlungu womwewu m’madera ena okwana 11 kuphatikizaponso ku Stanley Theater ku New Jersey (onani chithunzi pamwambapa). A Mboni za Yehova akuyembekezera kuti anthu onse amene adzasonkhane m’malo 11 amenewa adzapitirira 41,000.

Bambo J. R. Brown, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku likulu lawo ku Brooklyn ku New York, anati: “Anthu onse amene akufuna kubwera kumisonkhanoyi adzalandiridwa ndi manja awiri ndipo sadzanong’oneza bondo.” Misonkhanoyi yomwe izidzachitika kwa masiku atatu, idzakhala ndi nkhani zogwira mtima zofotokoza zimene Yesu anaphunzitsa zomwe zidzapindulitse achinyamata ndi achikulire omwe.

Misonkhano ya mutu wakuti “Tsanzirani Yesu ” imeneyi ipitirira kuchitika mpaka mu January 2016 ndipo ilipo pafupifupi 5,000 m’madera okwana 92. Misonkhanoyi yakonzedwa ndi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Mbali zonse kapena mbali zake zina za misonkhanoyi zidzachitika m’zinenero 347 kuphatikizaponso zinenero za manja zokwana 35.

Lankhulani Ndi:

Kuchokera ku Mayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000