Pitani ku nkhani yake

JUNE 1, 2016
UNITED STATES

A Mboni za Yehova Akugulitsa Nyumba Imene Inali Chuma Chawo Chapadera ku Brooklyn Yotchedwa The Towers

A Mboni za Yehova Akugulitsa Nyumba Imene Inali Chuma Chawo Chapadera ku Brooklyn Yotchedwa The Towers

Mmene nyumba yomwe ankaitcha kuti Towers Hotel inkaonekera atangoimanga kumene.

NEW YORK—Pa 24 May, 2016, a Mboni za Yehova anaika nyumba yawo ya nsanjika 16 yotchedwa The Towers, yomwe ili m’mphepete mwa msewu wotchedwa 21 Clark Street ku Brooklyn, pa mndandanda wa nyumba zimene akugulitsa. Nyumbayi yakhala zaka pafupifupi 90 ndipo kukula kwake ndi mamita 29,150 mbali zonse. Poyamba inali hotelo ndipo ndi yodziwika bwino chifukwa cha tinyumba tina 4 tomwe anatimanga pa denga lake.

Pulani yomangira nyumbayi anakonza ndi akatswiri ena otchuka a zomangamanga, a Starrett ndi a Van Vleck, omwe anamanganso sitolo zikuluzikulu za ku New York zotchedwa Lord & Taylor komanso Saks Fifth Avenue. Pa nthawi imene ankaitsegulira mu 1928, inali hotelo yotchedwa Leverich Towers. Patapita zaka zingapo, anthu ena anagula hoteloyi ndipo anaisintha dzina n’kukhala Towers Hotel. Nyumbayi ndi yokongola ndipo inali ndi chipinda chachikulu chovinila chokhala ndi nyale zikuluzikulu komanso malo ochezera pa denga lake. Munthu akakhala padengali amatha kuona mosavuta dera lotchedwa Lower Manhattan, doko lotchedwa New York Harbor komanso mlatho waukulu wotchedwa Brooklyn Bridge. Chifukwa cha zimenezi, nyumbayi inali imodzi mwa mahotelo otchuka kwambiri ku Brooklyn.

Masitepe okongola a m’nyumbayi okhala ndi zogwirira zofiirira m’mbali mwake komanso zipilala zozungulira zomwe zili ndi zithunzi zokongola.

Ngakhale kuti poyamba nyumbayi inali yokongola kwambiri, pofika m’ma 1970 siinkaonekanso bwino. Kenako a Mboni anagula nyumbayi pa 14 January, 1975. Pofika mu 1978, iwo anali ataisintha kuti ikhale ndi chipinda chodyera komanso zipinda zogona za a Mboni okwana 1,000 omwe amagwira ntchito ku likulu lawo la padziko lonse. A Richard Devine, omwe amalankhula m’malo mwa a Mboni anati: “Ntchito yathu yosindikiza mabuku inkakula kwambiri ndipo anthu ogwira ntchito ankaonjezerekanso. Choncho nyumbayi inatithandiza kwambiri chifukwa inali ndi malo okwanira okhala anthuwa.”

Malo ochezera omwe ali pa denga la nyumbayi. Munthu akakhala pa malowa n’kumayang’ana cha kumpoto, angathe kuona maofesi a likulu la a Mboni, milatho ya Brooklyn ndi Manhattan komanso imodzi mwa nyumba zazitali yotchedwa Empire State Building.

Kuyambira mu 1995, a Mboni anayamba ntchito yaikulu yokonzanso zinthu zosiyanasiyana zimene zinkakongoletsa nyumbayi zomwe zinawonongeka. Pofotokoza zokhudza ntchitoyi, bambo Devine ananena kuti: “Pofika m’ma 1990, tinali titamaliza kumanganso mkati mwa nyumbayi komanso kusintha chilichonse chokhudza za magetsi komanso madzi. Tinamanganso masitepe aakulu komanso okongola omwe anayambira cha kumene kuli malo odyera kukafika kumene kuli malo ofikira alendo.”

Bambo David A. Semonian omwe amalankhula m’malo mwa a Mboni ku likulu lawo ananena kuti: “Munthu akamayenda m’misewu ya m’dera la Brooklyn Heights n’kuyandikira nyumba ya The Towers, amachita chidwi kwambiri ndi kukongola kwake. Koma kupatula pa kukongola kwa nyumbayi kumene tayesetsa mwakhama kuti kukhalepobe, kwa zaka zambiri nyumbayi inali malo abwino kwambiri okhalamo anthu amene amagwira ntchito ku likulu lathu.”

Lankhulani ndi:

David A. Semonian, Office of Public Information, 1-718-560-5000