Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

JULY 10, 2013
UNITED STATES

A Mboni za Yehova Asaina Pangano Logulitsa Nyumba Zawo ku Brooklyn

A Mboni za Yehova Asaina Pangano Logulitsa Nyumba Zawo ku Brooklyn

NEW YORK—Pa July 5, 2013, a Mboni za Yehova anasainirana pangano ndi kampani ya RFR ndiponso ya Kushner Companies, kuti awagulitse nyumba zawo 5 zimene zili ku Brooklyn mumzinda wa New York, zomwe ankazigwiritsa ntchito posindikiza mabuku, komanso nyumba ina yogona yomwe ndi yosanjikizana ka 30. A Mboniwa ayamba kusamuka m’nyumbazi chaka chomwe chino m’mwezi wa August. Koma adzasamuka m’nyumba yogona ija m’chaka cha 2017.

Bambo David Semonian, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova wolankhula ndi atolankhani, anati: “Anthu ambiri a mumzinda uno wa New York City komanso alendo amene amadutsa pamlathowu, amaona chikwangwani chakuti ‘Tsiku ndi Tsiku Muziwerenga Mawu a Mulungu Omwe Ndi Baibulo Lopatulika’ ndiponso chakuti ‘Muziwerenga Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!’ Kwa zaka zambiri, m’nyumba zimenezi mwakhala mukuchitika ntchito yofunika kwambiri imene ikukhudza mbiri yathu komanso kupezeka kwathu ku Brooklyn kuno.” A Mboni akhala akugwiritsa ntchito nyumba 5 zimenezi posindikiza ndi kufalitsa Mabaibulo komanso mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo a m’zinenero zambirimbiri kwa zaka 77. Nyumba yoyambirira pa nyumba 5 zija anayamba kuigwiritsa ntchito m’chaka cha 1927. Ndipo mu 1937 anayamba kuwonjezera nyumba zina pamalopa. Pamene nyumba yogona yomwe ndi yosanja ka 30 ija inamangidwa, munkakhala anthu pafupifupi 1000 omwe ankagwira ntchito m’maofesi osindikizira mabuku omwe alinso pamalo omwewa.

A Mboni akugulitsa nyumbazi chifukwa akusamukira m’dera lina lakumpoto m’chigawo chomwechi cha New York. Ntchito yosamukayi inayamba mu 2004, pamene a Mboni za Yehova anasamutsa maofesi awo osindikiza ndi kutumiza mabuku m’mipingo, kuchoka ku Brooklyn kupita ku Wallkill, ku New York komweko. Panopa a Mboni ali ndi mapulani osamutsa likulu lawo kuchoka ku Brooklyn kupita ku Warwick, m’chigawo chomwechi cha New York, ndipo ntchito yomanga kumalo atsopanowa iyamba chakumapeto kwa chaka chino.

Bambo Semonian ananenanso kuti: “Timanyadira kwambiri tikaganizira za mbiri yathu ku Brooklyn. Takhala tikugwiritsa ntchito nyumba zimenezi pa ntchito yathu yofalitsa mabuku omwe amathandiza anthu ambiri padziko lonse lapansi. Koma tsopano tikuyembekezera mwachidwi maofesi athu atsopano ku Warwick, amene tidziwagwiritsa ntchito pa ntchito yathu yophunzitsa anthu uthenga wa m’Baibulo padziko lonse.”

Kuchokera m’mayiko ena:

Lankhulani ndi a J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000