Pitani ku nkhani yake

AUGUST 5, 2013
UNITED STATES

A Mboni Ayamba Ntchito Yomanga Likulu Lawo Latsopano ku Warwick, New York

A Mboni Ayamba Ntchito Yomanga Likulu Lawo Latsopano ku Warwick, New York

NEW YORK​—Lolemba pa July 29, 2013, a Mboni za Yehova anayamba ntchito yomanga nyumba ku Warwick, zomwe zikhale likulu lawo latsopano la padziko lonse. Ntchitoyi inayambika akuluakulu a boma atapereka chilolezo choti ntchitoyi iyambe.

Lachitatu pa July 17, akuluakulu onse a boma oona za mapulani a zomangamanga m’tauni ya Warwick anapereka chilolezo chomaliza chomwe chinali chofunika kwambiri kuti ntchitoyi iyambe, ndipo anachipereka atavomereza pulani ya a Mboni yomangira likulu lawo latsopano. Akuluakulu a bomawo anapereka chilolezochi patatha zaka 4 kuchokera pamene a Mboni anapeza malo ku Warwick pa July 17, 2009. Lachisanu pa July 26, a Mboni anapatsidwa chikalata choyamba chowapatsa mphamvu zoti akhoza kuyamba kumanga pamalowo ndipo Lolemba pa July 29, ntchito yokonza malowo ndiponso yokumba maziko inayambika.

A Mboniwo anali ofunitsitsa kuti asawononge zachilengedwe pomanga likulu lawolo ndipo zimenezi zinachititsa kuti akuluakulu onse a boma oona za mapulani a zomangamanga avomereze pulaniyo mosavuta. Mwachitsanzo, papulani yawoyo anakonza zoti amange khoma lothandiza kuti nthaka isamakokoloke komanso loteteza nyama zakutchire, monga njoka, kuti zisamafike pafupi ndi malowo.

Bambo Richard Devine, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova anati: “Tikusangalala kwambiri kuti tikugwira ntchito ndi akuluakulu a tauni ya Warwick ndiponso kuti ntchito yathu yomangayi ikuyenda bwino. Chilolezo chimene atipatsachi n’chofunika kwambiri pa ntchito yosamutsa likulu lathu ku Brooklyn kupita ku Warwick.” Nawonso Bambo Enrique Ford omwe ali mukomiti ya a Mboni yoyang’anira ntchito yomangayi pamodzi ndi Bambo Devine, ananena kuti: “Chikalata chimene akuluakulu a boma atipatsachi pamodzi ndi chilolezo choti tiyambe ntchito yomangayi chimene tinalandiranso mu July, n’zofunika kwambiri pokonza pulani ya kagwiridwe ka ntchito chifukwa tikufuna ntchito yonse yomangayi idzathe pakapita zaka 4.”

Poyamba malowo anali a kampani yotchedwa International Nickel kuyambira mu 1960 mpaka mu 1987, ndipo ankagwirapo ntchito zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, panali likulu la kampaniyi komanso ankachitirapo kafukufuku wa zinthu zosiyanasiyana. Patapita zaka 4 kampaniyi itachoka pamalowa, akuluakulu a koleji yotchedwa King’s College anagula malowa n’cholinga choti amangepo koleji. Koma izi sizinachitike ndipo pamalopo pakhala palibe aliyense kwa zaka zoposa 20 mpaka pamene a Mboni anawagula mu 2009.

Lankhulani ndi:

Kuchokera m’mayiko ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000