Pitani ku nkhani yake

MAY 31, 2013
UNITED STATES

A Mboni za Yehova Akonzanso Nyumba Yakalekale Yophunzirira Baibulo

A Mboni za Yehova Akonzanso Nyumba Yakalekale Yophunzirira Baibulo

NEW YORK​—⁠Pa April 13, 2013, a Mboni za Yehova anatsegulira nyumba yakalekale yotchedwa Stanley ku Jersey City, m’chigawo cha New Jersey pambuyo poikonzanso kwa miyezi 6. A Mboniwa akhala akugwiritsa ntchito nyumbayi popangira misonkhano yawo ikuluikulu kwa zaka pafupifupi 30. Ntchito yokonzayi yathandiza kuti nyumbayi ikhale malo abwino kwambiri ophunzirira Baibulo kwaulele.

M’nyumbayi aikamo mipando yatsopano ndipo zimenezi zathandiza kuti anthu oposa 250,000 omwe amakapangiramo misonkhano chaka chilichonse azikhala m’malo abwino. M’holo yake yaikulu ndiponso m’zipinda zake zina, aikamo zipangizo zapamwamba kwambiri zosonyeza mavidiyo, makamaka n’cholinga choti asonyeze mavidiyo a chinenero chamanja.

Anthu pafupifupi onse amene anagwira ntchitoyi ndi a Mboni za Yehova omwe anagwira mongodzipereka. Iwo anachokera m’madera osiyanasiyana a dziko la United States n’cholinga choti athandize nawo pokonza nyumba yakaleyo kuti izioneka ngati mmene inkaonekera idakali yatsopano.

Nyumbayi inamangidwa ku New Jersey kumapeto kwa zaka za m’ma 1920. Inali nyumba yaikulu kwambiri yoonetsera mafilimu m’dziko la United States. M’chaka cha 1978 nyumbayi inatsekedwa koma mu 1983, a Mboni za Yehova anagula nyumbayi n’kuyamba kuikonza. Iwo akhala akugwiritsira ntchito nyumbayi pophunzira Baibulo kuyambira 1985, chomwe ndi chaka chimene anaitsegulira.

Pothirira ndemanga pa ntchito yokonzanso nyumbayi yomwe yachitika posachedwa, J. R. Brown, yemwe analankhula m’malo mwa a Mboni za Yehova ananena kuti: “Ntchito yaikulu ya nyumbayi ndi kulambiriramo Yehova ndipo anthu a magulu a zinenero zoposa 15 amadzaphunzira Baibulo m’nyumbayi. Komabe anthu a ku New Jersey amasangalala kwambiri ndi nyumbayi chifukwa imawakumbutsa kale ndipo gulu lathu ndi losangalala kwambiri kuti takonzanso nyumba imene imakumbutsa anthu mbiri yakale.”

Mukhoza kulankhula ndi:

International: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000