Pitani ku nkhani yake

27 FEBRUARY, 2015
UNITED STATES

A Mboni Analandira Mphoto Chifukwa Chosamalira Zachilengedwe pa Ntchito Yawo Yomanga

A Mboni Analandira Mphoto Chifukwa Chosamalira Zachilengedwe pa Ntchito Yawo Yomanga

NEW YORK—A Mboni za Yehova, omwe amadziwika ndi ntchito yawo yophunzitsa anthu Baibulo, analandira mphoto chifukwa chomanga nyumba mwapamwamba kwambiri komanso m’njira yosawononga chilengedwe.

Bungwe lolimbikitsa anthu kumanga nyumba m’njira yosawononga chilengedwe (Green Building Initiative mwachidule GBI) ndi limene linapereka mphotoyi ku maofesi a Mboni za Yehova a ku United States m’dera la Wallkill, ku New York. Mphoto zomwe analandirazo zinali zokhudza mmene anamangira nyumba zawo ziwiri. Nyumba yoyamba ili kufamu ya Watchtower ndipo anamaliza kuimanga chakumapeto kwa chaka cha 2012. Nyumbayi imaoneka ngati chilembo cha F. Nyumba yachiwiri ilinso ku Wallkill komweko ndipo anaimanga kuti mukhale maofesi. Nyumbayi inamalizidwa mu 2014.

Maofesi a Mboni za Yehova ku Wallkill

A Shaina Sullivan, omwe amayang’anira zamalonda m’bungweli anati: “Padziko lonse pali nyumba zochepa kwambiri zomwe zinapatsidwa mphotoyi.” Mayi Sullivan ananenanso kuti nyumba yomwe mudzakhale maofesi a Mboni za Yehova ,yomwe ili ku Wallkill, “inamangidwa bwino kwambiri ndipo mumzinda wonse wa New York, nyumbayi ndi yapamwamba kwambiri kuposa nyumba zina zomwe zinalandira mphotoyi, zomwenso anazimanga kuti zikhale maofesi.” Nawonso a Jenna Middaugh, omwe ndi mkulu woyang’anira zomangamanga m’bungweli anati: “Pa nyumba 23 [za ku United States] zomwe zinapatsidwa mphoto ndi kampani yathu kungochokera mu 2006, nyumba yomwe mudzakhale maofesi a Mboni ku Wallkill ndi imene yachita bwino kwambiri kuposa zina zonse.”

Nyumba yooneka ngati chilembo cha F yomwe ili kumafamu a Watchtower

Bungwe la GBI limaona za ndalama zomwe zalowa kuti nyumba imangidwe komanso imapereka ziphaso zosonyeza kuti nyumba yamangidwa bwino. Limagwiranso ntchito ndi bungwe lina lomwe limayang’anira za zomangamanga komanso zolemba mapulani a nyumba zomangidwa m’njira yosawononga chilengedwe. Kumanga nyumba m’njira imeneyi si nkhani yamasewera chifukwa mukamalemba mapulani ake mumafunika kuonetsetsa kuti ntchito yomanga nyumbayo isadzakhale yowononga chilengedwe.. Mwachitsanzo mumafunika kupewa kuwononga madzi, magetsi, mpweya komanso kugwiritsa ntchito zipangizo zosawononga chilengedwe. Mumafunikanso kuonetsetsa kuti moyo wa anthu omwe azidzagwira ntchito m’nyumbayo isadzakhale pangozi.

Magetsi ena omwe ofesi ya ku Wallkill imagwiritsanso amapangidwa kuchokera ku mphamvu ya dzuwa, ndipo zimenezi ndi zimenenso zinachititsa kuti nyumbayi ilandire mphoto chifukwa chomangidwa mosawononga chilengedwe.

A David Bean, omwe ndi mkulu woyang’anira ntchito yomanga nyumba za Mboni za Yehova m’njira yosawononga chilengedwe ku United States, anati: “Mphoto zimene tapatsidwazi ndi umboni woti timayesetsa kupanga mapulani komanso kumanga nyumba zathu mwapamwamba kwambiri. Tikuyesetsanso kumanga bwino nyumba zathu zomwe zidzakhale likulu lathu m’dera la Warwick ku New York, ndipo n’kutheka zikhozanso kudzaikidwa m’gulu la nyumba zomangidwa bwino kwambiri.”

Akukonza denga loti akhoza kudzalapo maluwa komanso zinthu zina kumaofesi atsopano omwe ali mumzinda wa Warwick ku New York. Maofesiwa ndi amene adzakhale likulu la a Mboni za Yehova.

A Zeny St. Jean, omwe amayang’anira ntchito yomanga nyumba za a Mboni za Yehova padziko lonse ku malikulu athu anati: “Cholinga chathu chachikulu tikamachita zimenezi kumakhala kuthandiza kuti ntchito yophunzitsa anthu Baibulo iziyenda bwino. Tikuthokoza kwambiri kuti bungweli latipatsa mphoto zimenezi chifukwa choti tamanga nyumba m’njira yosawononga zinthu zachilengedwe ndipo tipitirizabe kuyesetsa kumanga nyumba mwa njira imeneyi padziko lonse.”

Yankhulani ndi:

Kuchokera M’mayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000