A Mboni za Yehova akuyesetsa kuthandiza a Mboni anzawo komanso anthu ena omwe anakhudzidwa ndi mvula yamkuntho yotchedwa Hurricane Matthew. Mvula yamkunthoyi inagwa kumayambiriro kwa mwezi wa October 2016. Madera omwe anakhudzidwa ndi mvulayi ndi Bahamas, Caribbean komanso kum’mwera chakum’mawa kwa United States.

Ku Bahamas kuli a Mboni za Yehova 1,400 ndipo 700 anakhudzidwa ndi mvula yamkunthoyi. Pofuna kuthandiza anthuwa zinthu monga zakudya komanso madzi zinatumizidwa mwamsanga m’madera awiri a dzikoli.

Ku Cuba nyumba 124 za a Mboni zinawonongeka ndipo nyumba zokwana 31 zinagweratu.

A Mboni oposa 700 ku Haiti anathawa m’nyumba zawo chifukwa cha mvula yamkunthoyi. Nyumba 73 za a Mboni komanso malo awo 4 olambirira anagweratu. Kuwonjezera apo, nyumba 274 komanso malo 15 olambirira zinawonongeka. Chakudya ndiponso mankhwala zinaperekedwa kwa anthu amene anakhudzidwa ndi ngoziyo komanso anagula matenti kuti anthu amene nyumba zawo zinagweratu akhalemo mongoyembekezera.

Ku United States, mvulayi inawononga nyumba 125 za anthu a Mboni. Malipoti anasonyeza kuti anthu ankaopa kwambiri poganiza kuti madzi angasefukire chifukwa cha mitsinje imene inali itadzaza kwambiri.

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova limayang’anira ntchito yopereka chithandizo kwa anthu omwe akhudzidwa ndi ngozi. Bungweli limagwiritsa ntchito ndalama zomwe anthu amapereka mwakufuna kwawo pofuna kuthandiza ntchito yolalikira padziko lonse. A David A. Semonian, omwe amayankhula m’malo mwa a Mboni za Yehova ananena kuti: “Ngakhale kuti palibe wa Mboni amene anafa pangoziyi, tikumvera chisoni anthu onse omwe achibale awo amwalira pangoziyi.”

Lankhulani ndi:

Padziko Lonse: David A Semonian, Office of Public Information, 1-718-560-5000

Bahamas: Maxwell Dean, 1-242-422-6472

Haiti: Daniel Lainé, 509-2813-1560