Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

MAY 13, 2014
UNITED STATES

Mphepo Yamkuntho Yasakaza M’dera la Pakati ndi Kum’mwera M’dziko la United States

Mphepo Yamkuntho Yasakaza M’dera la Pakati ndi Kum’mwera M’dziko la United States

Pa April 27, 2014, mphepo yamkuntho inasakaza zinthu kwambiri m’chigawo chapakati ndi kum’mwera m’dziko la United States. Mphepo yamkunthoyi inawononga nyumba zambiri ndipo malipoti akusonyeza kuti anthu 30 anafa. Akuluakulu a ku ofesi ya Mboni za Yehova ku United States ananena kuti palibe munthu wa Mboni amene wafa kapena kuvulala pa ngoziyi. Komabe nyumba 7 za anthu a Mboni zawonongeka. Kuwonjezera pamenepa, nyumba zitatu zolambiriramo za a Mboni zawonongeka ndi mphepoyi. Padakali pano, anthu a Mboni za Yehova m’derali akonza makomiti amene akuthandiza anthu omwe akhudzidwa ndi ngoziyi.

Lankhulani ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000