Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

5 AUGUST, 2016
UNITED STATES

A Mboni za Yehova Agulitsa Nyumba Zimene Zinali Likulu Lawo ku Brooklyn

A Mboni za Yehova Agulitsa Nyumba Zimene Zinali Likulu Lawo ku Brooklyn

NEW YORK—Pa 3 August, 2016, a Mboni za Yehova anagulitsa nyumba zomwe zinali likulu lawo padziko lonse. Nyumbazi zili ku 25/30 Columbia Heights ku Brooklyn, mumzinda wa New York ndipo azigulitsa ku makampani a Kushner omwe ali pa mgwirizano ndi kampani ya LIVWRK. Zimenezi zikusonyeza kuti a Mboni za Yehova ayamba kusamukira kumalo awo atsopano omwe ali ku Warwick, mumzinda wa New York.

Malo amene awagulitsawa ndi aakulu masikweya mita 68,154, ndipo akuphatikizapo nyumba zikuluzikulu ziwiri zomwe zili pakati pa madera otchuka kwambiri omwe ndi Brooklyn Heights, Fulton Ferry komanso Dumbo. Nyumba zina zimene akuzigulitsa ndi zomwe zagundana ndi nyumba za 25/30 Columbia Heights zomwe ndi za 50 Columbia Heights, 58 Columbia Heights komanso 55 Furman Street. Nyumba zonsezi zili pafupi ndi Brooklyn Bridge.

Nyumba za 50 Columbia Heights ndi 58 Columbia Heights

Nyumba ya 55 Furman Street

A Mboni za Yehova anagula nyumba yomwe ili ku 25/30 Columbia Heights ku kampani ina yopanga mankhwala ya E.R. Squibb & Sons, yomwe panopa ndi mbali ya Bristol-Myers Squibb. Nyumba zimenezi zimaonekera patali kwambiri chifukwa cha chikwangwani chosonyeza nthawi komanso mmene kukutenthera chomwe chili pamwamba pa nyumba ya 30 Columbia Heights. Chikwangwani chomwe poyamba chinalembedwa kuti “Squibb” anachisintha pamene ankagula nyumbazi mu 1969 ndipo chinalembedwa kuti “Watchtower.” A Richard Devine, omwe amayankhula m’malo mwa a Mboni za Yehova, ananena kuti: “Chifukwa chimene tagulitsira nyumbazi n’choti tikufuna malo otakasuka popeza ntchito zathu zikuwonjezeka. Kuwonjezera pamenepa, nyumba zathu zinangoti balala mumzinda wa Brooklyn, ndiye tikufuna kuti zonse zikhale malo amodzi.”

A David A. Semonian, omwe amalankhula m’malo mwa a Mboni za Yehova kulikulu lathu, anati: “Nyumba za 25/30 Columbia Heights ndi zosaiwalika pa mbiri yathu ndiponso pa mbiri ya dera lonse la Brooklyn.”

Lankhulani Ndi:

David A. Semonian, Ofesi ya Nkhani, 1-718-560-5000