LVIV, ku Ukraine—Pa 14 February 2015, a Mboni za Yehova ku Ukraine anakonza msonkhano wapadera n’cholinga choti alimbikitse Akhristu anzawo oposa 17,000 omwe amakhala m’dera limene kunali nkhondo kum’mawa kwa dzikoli. Msonkhano wa maola awiriwu unaulutsidwa kumadera osiyanasiyana a ku Ukraine kuchokera ku ofesi ya Mboni za Yehova mumzinda wa Lviv. Anachita zimenezi pogwiritsa ntchito Intaneti. Msonkhanowu unali wapanthawi yake chifukwa pa 24 January 2015 nyumba 61 za a Mboni zinawonongedwa ndi mabomba amene anaphulitsidwa mumzinda wa Mariupol. Wa Mboni wina anavulazidwa kwambiri ndipo wina wazaka 16 anaphedwa.

Anthu akusonkhana m’Nyumba ya Ufumu ya mumzinda wa Makiyivka, womwe uli m’dera limene kuli nkhondo, kuti aonere msonkhano kuchokera ku ofesi ya ku Ukraine.

Mogwirizana ndi ofesi ya ku Russia, ofesi ya ku Ukraine inakonza zoti ajambule vidiyo ya msonkhano wonse kenako n’kuiulutsa kwa a Mboni a ku Belarus ndi ku Russia. Izi zinathandiza kuti a Mboni ena 186,258 a ku Belarus ndi ku Russia aonerenso msonkhanowo kuwonjezera pa anthu 150,841 amene anaonera ku Ukraine. Chiwerengero cha a Mboni onse amene anaonera msonkhanowu chinali 337,099.

Mneneri wa Mboni za Yehova ku Ukraine dzina lake Gustav Berki anati: “Zimene anafotokoza pamsonkhanowu zokhudza mmene ntchito yopereka chithandizo ikuyendera ku Ukraine zinalimbikitsa kwambiri anthu am’dera limene kuli nkhondo. Anthu analimbikitsidwanso kwambiri atamva kuti komiti yopereka chithandizo ya mumzinda wa Rostov-on-Don ku Russia ikusamalira bwino anzathu amene anathawa kwawo.”

Mneneri wa Mboni za Yehova ku Russia dzina lake Yaroslav Sivulskiy anati: “A Mboni za Yehova amadziwika padziko lonse kuti ndi anthu amtendere ndipo salowerera ndale. Pamsonkhanowu panafotokozedwa mfundo za m’Baibulo zimene zimachititsa kuti a Mboni asamalowerere ndale. Izi zinasonyeza chifukwa chake a Mbonife, kaya ndife a ku Russia, ku Ukraine kapena dziko lina lililonse, sitimenya nawo nkhondo.”

A Mboni awiri a mumzinda wa Horlivka m’dera la Donetsk anapulumuka bomba litawomba nyumba yawo iwo ali momwemo.

Pofika panopa makomiti opereka chithandizo amene ofesi ya ku Ukraine yakhazikitsa kuti asamalire anthu okhudzidwa ndi nkhondoyi akwana 14. Makomitiwa apereka chakudya choposa matani 149 ndiponso zovala zoposa matani 21 kwa a Mboni anzawo komanso anthu ena a m’derali. Athandizanso anthu othawa kwawo oposa 7,600 kuti apeze pokhala ndipo akonza kapena kumanganso nyumba za anthu ndiponso Nyumba za Ufumu (malo olambirira) zomwe zinawonongeka. Mwachitsanzo, patangodutsa masiku awiri kuchokera pamene mabomba anaphulitsidwa mumzinda wa Mariupol, komiti ina yopereka chithandizo inakwanitsa kupeza anthu ongodzipereka okwana 160 kuti akonze nyumba 34 zimene zinawonongeka.

Bomba linaphulitsidwa pamalo oimika magalimoto amene ali pafupi ndi Nyumba ya Ufumu (yomwe sikuoneka) mumzinda wa Mariupol.

A Berki anafotokozanso kuti ofesi ya ku Ukraine simangopereka chithandizo cha chakudya ndi malo ogona chokha koma imathandizanso anthu mwauzimu. Iye anati: “Kuwonjezera pa msonkhanowo, pali anthu ena amene amayendera malo 136 kumene a Mboni za Yehova amapezeka m’dera limene kuli nkhondoko kuti akawalimbikitse ndi Mawu a Mulungu. Mofanana ndi zimene zimachitika m’mipingo ya Mboni za Yehova padziko lonse, akulu a m’mipingo imene ili m’derali akuthandiza ndiponso kulimbikitsa anthu a m’mipingo yawo ndi Mawu a Mulungu.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 500

Belarus: Pavel Yadlouski, tel. +375 17 292 93 78

Russia: Yaroslav Sivulskiy, tel. +7 812 702 2691

Ukraine: Gustav Berki, tel. +38 032 240 9323