Pitani ku nkhani yake

JULY 18, 2014
UKRAINE

Lipoti Lokhudza Mboni za Yehova ku Ukraine ndi ku Crimea

Lipoti Lokhudza Mboni za Yehova ku Ukraine ndi ku Crimea

LVIV, Ukraine—Ofesi ya Mboni za Yehova ku Ukraine yanena kuti pa June 17, 2014, munthu mmodzi wa Mboni anafa kum’mawa kwa mzinda wa Kramatorsk bomba litaphulika pafupi ndi galimoto yake. Kupatula pa munthu mmodziyu, palibenso wa Mboni amene wamwalira kapena kuvulala kwambiri chifukwa cha nkhondo yomwe inayamba miyezi ingapo yapitayi m’dzikoli. Komabe a Mboni ambiri anasamutsidwa m’madera a kum’mawa kwa dziko la Ukraine komwe kwakhudzidwa kwambiri ndi nkhondo. Anthuwa akukhala m’nyumba za a Mboni anzawo.

A Mboni za Yehova ku Ukraine akupitirizabe kuuza anthu uthenga wa m’Baibulo, womwe ndi wotonthoza, ngakhale kuti m’dzikoli mukuchitika ziwawa. Chakumayambiriro kwa mwezi wa June 2014, a Mboni za Yehova anachita misonkhano yambiri mwamtendere kum’mawa kwa dziko la Ukraine. Pa misonkhanoyi, ankakamba nkhani za m’Baibulo komanso zitsanzo zosonyeza mmene tingagwiritsire ntchito malangizo a m’Baibulo pamoyo wathu. Anthu oposa 5,200 anapezeka pamisonkhanoyi. A Mboni akuyembekezera kupanga misonkhano yachigawo pafupifupi 40 ku Ukraine ndi ku Crimea. Nkhani zimene zidzakambidwe pamisonkhanoyi zidzafotokoza zimene Baibulo limanena, zakuti anthu adzakhala mwamtendere Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira. Anthu oposa 165,000 akuyembekezeka kudzapezeka pamisonkhanoyi ku Ukraine komanso 7,500 ku Crimea.

Kuchokera m’mayiko ena:

Lankhulani ndi: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Ukraine: Vasyl Kobel, tel. +38 032 240 9323