Pitani ku nkhani yake

NOVEMBER 21, 2014
UKRAINE

A Mboni za Yehova Akuthandiza Anthu Ambiri Amene Akusowa Pokhala ku Ukraine

A Mboni za Yehova Akuthandiza Anthu Ambiri Amene Akusowa Pokhala ku Ukraine

LVIV, Ukraine—A Mboni za Yehova akupitiriza kuthandiza a Mboni anzawo omwe akusowa pokhala chifukwa cha nkhondo imene yavuta kum’mawa kwa dziko la Ukraine.

A Mboni pafupifupi 7,500 anathawa m’madera amene kukuchitika nkhondo. Ndipo ofesi ya Mboni za Yehova ku Lviv inakhazikitsa makomiti 7 omwe akusamalira anthu pafupifupi 4,000 mwa a Mboni amenewa. Pamene a Mboni pafupifupi 3,500 akukhala m’nyumba za achibale awo komanso a Mboni anzawo a ku Ukraine ndi ku Russia. Makomiti ena 6 akusamalira a Mboni oposa 17,500 amene akukhalabe kumene kukuchitika nkhondo.

Mabomba anawononga nyumba zambiri za a Mboni, ndipo iyi ndi imodzi mwa nyumbazi. Nyumbayi ili m’mudzi wotchedwa Semenivka, m’chigawo cha Donetsk.

Ofesi ya Mboni za Yehova ku Lviv inanena kuti a Mboni za Yehova 6 anaphedwa ndi mabomba chiyambireni nkhondoyi. Pa June 17, 2014, wa Mboni mmodzi wa ku Kramatorsk anaphedwa ndi bomba limene linaphulika pafupi ndi galimoto yake. Mabomba anaphanso a Mboni 5 omwe ankakhala m’mizinda yotchedwa Donetsk, Sloviansk, Rozkishne, ndi Luhansk.

Ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Lviv ikugwira ntchito yomanganso malo olambiriramo a Mboni za Yehova komanso nyumba zawo.

A Mboni za Yehova akukonza denga la nyumba yomwe inawonongeka mumzinda wa Sloviansk.

Lankhulani ndi:

Kuchokera M’mayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Ukraine: Vasyl Kobel, tel. +38 032 240 9323