Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

JANUARY 31, 2017
THAILAND

Akuluakulu a Boma la Thailand Akugwiritsa Ntchito Mabuku a Mboni za Yehova Pothandiza Anthu a M’dziko Lawo

Akuluakulu a Boma la Thailand Akugwiritsa Ntchito Mabuku a Mboni za Yehova Pothandiza Anthu a M’dziko Lawo

BANGKOK—Akuluakulu a boma ku Thailand akugwiritsa ntchito mabuku a Mboni za Yehova pophunzitsa anthu pa nkhani monga kulera ana, kupewa nkhanza m’banja, kukhala osangalala komanso athanzi. Pofika mwezi uno, akuluakuluwa akhala akugwiritsa ntchito mabukuwa kwa zaka zitatu.

Boma la ku Thailand lakonza zoti anthu aziphunzitsidwa kumalo a maphunziro okwana 8,700 m’dzikoli. Kuwonjezera pamenepa, boma lakonzanso kuti pakhale malo ena 11 kumene atsogoleri osiyanasiyana akuphunzitsidwa. Pa chithunzi chili pamwambapa, yemwe ali pakatiyo ndi Chaiwat Saengsri ndipo ndi mtsogoleri wa malo oterewa omwe ali kudera la Nakhon Nayok, kumpoto chakum’mawa kwa Bangkok. Iye anati: “Ndimasangalala ndi a Mboni za Yehova chifukwa chakuti cholinga cha ntchito yawo ndi kuthandiza anthu kuti adziwe Mlengi wathu. Tili ndi cholinga chofanana ndi chawo chothandiza anthu kuti azikhala mwamtendere ndiponso osangalala chifukwa chokhala ndi mkhalidwe abwino.” Iye anawonjezera kuti: “Mwachitsanzo, m’nkhani ya mu Galamukani! yakuti ‘Kodi Mungapewe Bwanji Kulankhula Mawu Achipongwe?’ muli mfundo zimene bungwe loona za chitetezo komanso kuthandiza anthu kuti azigwirizana likuyesetsa kuphunzitsa atsogoleri a m’dzikoli. Nkhaniyi inatithandiza kwambiri pophunzitsa atsogoleriwa.” A Chaiwat anapempha a Mboni kuti iye ndi anzake agwiritse ntchito mabuku awo pochita msonkhano umene anapanga ndi alangizi 20 komanso atsogoleri 100 ochokera m’madera 28 a m’dzikoli. Kumsonkhanowu anaphunzitsidwa zimene angachite kuti azitsogolera bwino komanso kuthandiza anthu kuti azigwirizana. Chithunzi chili pamwambapa chikusonyeza a Chaiwat limodzi ndi a Mboni.

Munthu wina amene amalankhula moimira Mboni za Yehova ku Thailand dzina lake Anthony Petratyotin ananena kuti: “Tikusangalala kwambiri kudziwa kuti atsogoleri a m’dzikoli akugwiritsa ntchito malangizo ochokera m’Baibulo amene ali m’mabuku athu. Tipitiriza kuwapatsa akuluakulu a boma mabuku athu komanso kuwafalitsa kwa anthu ambiri ngati mmene timachitira nthawi zonse.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera m’mayiko ena: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Thailand: Anthony Petratyotin, +66-2-375-2200