Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

8 JULY, 2016
SRI LANKA

A Mboni za Yehova Anathandiza Anthu M’dziko la Sri Lanka Mutagwa Chimvula Choopsa

A Mboni za Yehova Anathandiza Anthu M’dziko la Sri Lanka Mutagwa Chimvula Choopsa

A Mboni za Yehova akulongedza katundu woti akagawire anthu omwe akhudzidwa ndi ngoziyi.

COLOMBO, Sri Lanka—M’chigawo chapakati chamapiri a Aranayaka, chomwe chili pamtunda wa makilomita 100 kuchokera ku Colombo lomwe ndi likulu la dzikoli, kunagwa chimvula choopsa. Chimvulachi chinachititsa kuti nthaka ikhute madzi moti inafewa kwambiri n’kuyamba kuyenda ndipo inakwirira midzi ingapo n’kupha anthu oposa 100. Zimenezi zinachititsanso kuti anthu okwana 350,000 asowe pokhala. Mvulayi inayamba kugwa pa 15 May ndipo pa nthawi ina inkakhuthuka koopsa. Mwachitsanzo, m’tauni ya Kilinochchi, pa maola 24 okha mvulayi inagwa mamilimita 373. Akuluakulu a boma ananena kuti imeneyi inali ngozi yoopsa kwambiri yomwe inali isanachitikeponso, kungochokera pamene ku Sri Lanka kunachitika tsunami m’chaka cha 2004.

Ofesi ya Mboni za Yehova ku Sri Lanka inanena kuti palibe wa Mboni za Yehova amene anafa pangoziyi. Komabe, nyumba za a Mboni pafupifupi 200 zinawonongekeratu moti ankasowa pokhala. Nyumba ya Ufumu, kapena kuti nyumba imene a Mboni za Yehova amalambiriramo, ku Kaduwela ili pamtunda wa makilomita 15 kuchokera m’tauni ya Colombo. M’nyumbayi munadzaza madzi moti anangotsala pang’ono kufika kudenga.

A Mboni za Yehova akulongedza katundu woti akagawire anthu omwe akhudzidwa ndi ngoziyi.

A Mboni za Yehova anakhazikitsa komiti yoti ithandize anthu amene anakhudzidwa ndi ngoziyi. Anakonza zoti agawe zakudya ndi zinthu zina kwa anthuwo komanso kuwalimbikitsa ndi Mawu a Mulungu. Nyumba ya Ufumu ya ku Kotahena ndi imene ankasungirako chakudya, madzi, zovala komanso mankhwala. A Mboni ambiri anadzipereka kugawa zinthu zimenezi kwa a Mboni anzawo komanso anthu ena amene anakhudzidwa ndi ngoziyi.

A Nidhu David, omwe amayankhula m’malo mwa a Mboni za Yehova ku Sri Lanka, anati: “Tipitirizabe kupempherera anthu omwe akhudzidwa ndi ngoziyi. Tipitiriza kuwapatsa zakudya, zovala komanso zinthu zina. Tikufunitsitsanso kupitirizabe kuthandiza nawo kuchotsa matope m’nyumba zomwe zinakwiririka pangoziyi. Timadziwa kuti mutu umodzi susenza denga, n’chifukwa chake tikuyesetsa kuthandiza anthu omwe akuvutika chifukwa cha ngoziyi.”

Lankhulani Ndi:

Padziko Lonse: David A. Semonian, Ofesi ya Nkhani, 1-718-560-5000

Sri Lanka: Nidhu David, 94-11-2930-444