A Mboni za Yehova akugwira ntchito yothandiza anzawo komanso anthu ena omwe anakhudzidwa ndi ngozi ya kusefukira kwa madzi komanso kugumuka kwa nthaka. Ngoziyi inachitika kum’mwera komanso kumadzulo kwa dziko la Sri Lanka chifukwa cha mvula yomwe inayamba pa 26 May. Malipoti akusonyeza kuti anthu oposa 200 anamwalira pangoziyi komanso ena oposa 77, 000 akusowa pokhala.

Ofesi ya Mboni za Yehova ku Sri Lanka inakonza makomiti awiri opereka chithandizo kuti akathandize abale awo oposa 100 omwe anakhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi. Komitiyi ikugwira ntchito yopereka chakudya komanso kupezera anthuwo malo okhala. Pangoziyi palibe wa Mboni aliyense amene anamwalira.

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova limayang’anira ntchito yothandiza anthu amene akhudzidwa ndi ngozi zadzidzidzi kuchokera kulikulu lawo ku Warwick, New York. Bungweli limagwiritsa ntchito ndalama zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo pofuna kuthandiza pa ntchito yolalikira padziko lonse.

Lankhulani ndi:

Padziko Lonse: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Sri Lanka: Nidhu David, +94-11-2930-444