Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

FEBRUARY 14, 2014
SOUTH KOREA

Kafukufuku Wasonyeza Kuti Anthu a ku South Korea Akufuna Kuti Anthu Okana Kulowa Usilikali Azipatsidwa Ntchito Zina

Kafukufuku Wasonyeza Kuti Anthu a ku South Korea Akufuna Kuti Anthu Okana Kulowa Usilikali Azipatsidwa Ntchito Zina

SEOUL, Korea—Kafukufuku waposachedwapa amene bungwe lina linachita ku South Korea, anasonyeza kuti anthu ambiri a m’dzikolo akufuna kuti boma lizipereka ntchito zina kwa anthu amene akana kulowa usilikali m’malo moti azimangidwa. Kuyambira pa November 4 mpaka pa 7, 2013, amuna komanso akazi a ku Korea okwana 1,211 anafunsidwa pa kafukufukuyu. Zotsatira zake zinasonyeza kuti anthu 68 pa 100 alionse akufuna kuti anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira azipatsidwa ntchito zina m’malo moti azimangidwa. Zimene apeza pa kafukufukuyu zikusonyeza kuti anthu ambiri asintha maganizo awo, poyerekezera ndi kafukufuku wina amene anachitika mu 2008. Pa kafukufuku wa mu 2008 ameneyo anapeza kuti anthu 29 okha pa 100 alionse ankafuna kuti anthu okana kulowa usilikali azipatsidwa ntchito zina.

Zikuonekanso kuti anthu ena a zamalamulo ku Korea akufuna kuti anthu amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira azipatsidwa ntchito zina m’malo moti boma liziwamanga. Pulofesa wina dzina lake Han In-seop wa pa yunivesite ina yophunzitsa za malamulo yotchedwa Seoul National, analemba nkhani ya mutu wakuti: “Mavuto Okhudzana ndi Kukana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Zimene Munthu Amakhulupirira.” M’nkhaniyo, iye anati: “Palibe woweruza mlandu aliyense amene angafotokoze bwinobwino kuti anthu amene amakana kulowa usilikali amaphwanya malamulo ati. Anthu amene amamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali sapatsidwa chikalata chowadziwitsa malamulo amene aphwanya. Boma limachita zimenezi podziwa kuti omangidwawo sangathawe. Pambuyo pa chigamulo chilichonse chimene amapereka, oweruza milandu amavutika maganizo komanso zimawakhudza kwambiri.”

Bungwe Loona za Ufulu wa Anthu ku Korea linatulutsa filimu yomwe muli nkhani yokhudza kumangidwa kwa anthu amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Mufilimuyi muli kachigawo kena kotchedwa “Ice River,” komwe kamasonyeza wa Mboni za Yehova amene anakana kulowa usilikali. Yemwe anatsogolera popanga filimuyi anafotokoza kuti anaganiza zopanga filimuyi chifukwa a Mboni za Yehova ambiri amamangidwa chaka chilichonse chifukwa chokana kulowa usilikali. Mogwirizana ndi lipoti limene nthambi ya bungwe la United Nations yoona za ufulu wachibadwidwe linatulutsa mu June 2013, zikusonyeza kuti anthu 93 pa 100 alionse a Mboni za Yehova amene anamangidwa padziko lonse chifukwa chokana kulowa usilikali, ndi a m’dziko la Korea.

Lankhulani ndi:

Kuchokera m’mayiko ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Republic of Korea: Dae-il Hong, tel. +82 31 690 0055