NEW YORK—Pa 31 May, 2017, mtsogoleri wa dziko la Russia, a Vladimir Putin, anapereka mphoto (Order of “Parental Glory”) kwa a Valeriy ndi a Tatiana Novikkwa omwe ndi a Mboni za Yehova ndipo amakhala ku Karelia. Iwo anapatsidwa mphotoyi chifukwa cholera bwino ana awo 8 ndipo mwambo wopereka mphoto imeneyi unachitikira kunyumba ya boma mumzinda wa Moscow.

Mwambo wopereka mphotoyi unachitikira kunyumba ya boma patsiku limenenso mayiko padziko lonse amakumbukira za kusamalira ana.

Mtsogoleri wadziko la Russia ndi amene analamula mu May 2008 kuti makolo amene akulera bwino ana awo azipatsidwa mphotoyi. Boma la Russia limapereka mphoto imeneyi kwa makolo amene alera bwino kwambiri ana osachepera 7. Limapereka mphotoyi kwa makolo okhawo amene achita bwino kwambiri posamalira ana awo kuti akhale athanzi labwino, kuwaphunzitsa bwino komanso kuwasamalira kuti akule bwino ndiponso kuti akhale ndi makhalidwe abwino. Makolo amene apatsidwa mphoto imeneyi amaonedwa kuti ndi chitsanzo chabwino choti mabanja ena atengere.

A Valeriy Novik, omwe ali ndi ana 8 akulandira mphoto kuchokera kwa pulezidenti Putin.

A David . Semonian omwe amalankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku likulu lawo lapadziko lonse anati: “Tikuona kuti mphoto imeneyi ndi umboni wosonyeza kuti maphunziro aulere amene a Mboni za Yehova amapereka amathandiza makolo komanso ana awo kuti akhale nzika zodalirika ku Russia komanso padziko lonse. Tikukhulupirira kuti mphoto imene pulezidenti Putin wapereka adzaiganizira bwino pa 17 July, 2017, pomwe Khoti Lalikulu Kwambiri M’dziko la Russia lidzaunikenso chigamulo chomwe linapereka, chakuti likulu lathu m’dziko la Russia litsekedwe.”

Lankhulani ndi:

David David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000