Pitani ku nkhani yake

21 MARCH, 2017
RUSSIA

A Mboni za Yehova Padziko Lonse Akulimbikitsidwa Kulemba Makalata Opempha Kuti Boma la Russia Lisaletse Ntchito Yawo M’dzikolo

NEW YORK—Boma la Russia laopseza kuti liletsa ntchito ya Mboni za Yehova m’dzikolo. Choncho a Mboni za Yehova padziko lonse aganiza zolemba makalata opita ku boma la Russia ndiponso kwa akuluakulu a Khoti Lalikulu m’dzikolo. Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova likupempha a Mboni opitirira 8,000,000 padziko lonse kuti alembe nawo makalatawa.

Pa 15 March, 2017, Unduna Woona Zachilungamo m’dziko la Russia unakapereka chisamani ku Khoti Lalikulu la m’dzikolo choti liike Ofesi ya Nthambi ya Mboni za Yehova m’dzikolo pa gulu la mabungwe amene amachita zoopsa komanso kuti ofesiyo itsekedwe. Undunawo ukufunanso kuti ntchito zonse zimene ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova imagwira ziletsedwe. Ngati Khoti Lalikulu lingagwirizane ndi zimene undunawu wanena, ndiye kuti likulu la Mboni za Yehova la m’dzikolo lomwe lili pafupi ndi mzinda wa St. Petersburg litsekedwa. Komanso zimenezi zingapangitse kuti mabungwe okwana 400 amene amaimira Mboni za Yehova m’dzikolo athetsedwe ndiponso kuti mipingo yopitirira 2,300 ya Mboni za Yehova isaloledwenso kugwira ntchito zawo. Boma la Russia likhozanso kulanda ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova m’dzikolo komanso nyumba zimene a Mboni amagwiritsa ntchito polambira. Kuwonjezera pamenepo, wa Mboni aliyense akhoza kumazengedwa mlandu chifukwa chochita zinthu zokhudza kulambira. Khoti Lalikulu likuyembekezeka kupereka chigamulo chake pa 5 April.

A David A. Semonian, omwe amayankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku likulu lawo ku America, ananena kuti: “Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova likufunitsitsa kuti a Mboni za Yehova ku Russia athandizidwe mwamsanga. Kuzenga mlandu anthu amtendere komanso omwe amatsatira malamulo ngati kuti ndi zigawenga, n’kulakwa ndiponso n’kusamvetsa lamulo lothana ndi magulu oopsa. Choncho, milandu yotereyi imakhala yopanda zifukwa zomveka.”

Aka si koyamba kuti a Mboni za Yehova padziko lonse alembe makalata oterewa. Tikutero chifukwa chakuti zaka pafupifupi 20 zapitazo, akuluakulu ena a boma la Russia pa nthawiyo ankayesetsa kuchita zinthu zoipitsa mbiri ya Mboni za Yehova. Choncho, a Mboni za Yehova padziko lonse analemba makalata pofuna kuteteza Akhristu anzawo a ku Russia. Komanso a Mboni za Yehova analembaponso makalata opempha akuluakulu a boma kuti asiye kuzunza a Mboni a m’mayiko ena, monga dziko la Jordan, Korea, ndi Malawi.

A Semonian ananenanso kuti: “Kuwerenga Baibulo, kuimba ndiponso kupemphera limodzi ndi Akhristu anzathu si mlandu. Ndipo tikukhulupirira kuti makalata omwe a Mboni padziko lonse tingalembe athandiza akuluakulu a boma la Russia kuti asaletse Akhristu anzathu kulambira m’dzikolo.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Russia: Yaroslav Sivulskiy, +7 812 702 2691