Nkhaniyi ndi yachiwiri pa nkhani zitatu zomwe zikufotokoza zimene ananena akatswiri a zachipembedzo, a zandale, zachikhalidwe cha anthu komanso a maphunziro a ulamuliro wa Soviet Union.

ST. PETERSBURG, Russia—Akuluakulu a boma ku Russia akufuna kuti Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lomwe limafalitsidwa ndi a Mboni za Yehova, lisapezekenso m’dzikomo. Akuluakuluwa akunena kuti Baibuloli lili m’gulu la “zinthu zoopsa.”

Dr. Ekaterina Elbakyan

Dr. Ekaterina Elbakyan, yemwe ndi pulofesa woona za chikhalidwe cha anthu payunivesite ina ku Moscow anati: “Ngati khoti lingagamule kuti Baibuloli liletsedwe, ndiye kuti “liphwanya lamulo la boma lokhudza zinthu zoopsa pa Gawo 3, lomwe a Putin omwe ndi mtsogoleri wa dzikolo, anasainira m’chaka cha 2015.” Lamulo lomwe lili pa gawoli limati: “Kugwiritsa ntchito mawu a m’Baibulo, Quran, Tanakh komanso Kangyur, sikungakhale kugwiritsa ntchito zinthu zoopsa.”

Dr. Roman Lunkin

Dr. Roman Lunkin yemwe ndi mtsogoleri wa zachipembedzo komanso za chikhalidwe cha anthu ananena kuti: “Kodi ngati munthu wina angaganize zoletsa kugwiritsa ntchito mawu ena a m’buku lopatulika, si ndiye kuti mabuku ena onse opatulikawa aletsedwanso? Ndipotu a Mboni za Yehova ndi amene ayamba kuvutika ndi nkhani imeneyi chifukwa cha Baibulo lawo.”

Dr. Jeffrey Haynes

Kuwonjezera pamenepo, Dr. Jeffrey Haynes yemwe ndi pulofesa pa nkhani zandale komanso mtsogoleri wa zamaphunziro achipembedzo payunivesite ina ku London, ananena kuti: “Boma la Russia linasainira nawo Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale. Ngati dziko la Russia lingaletse Baibuloli, ndiye kuti bomali lidzakhala likuphwanyira anthu ufulu wachipembedzo.”

Mlandu wokhudza Baibulo la Dziko Latsopano ukuzengedwera m’khoti la mzinda wa Vyborg womwe uli pamtunda wa makilomita 138 kumpoto chakumadzulo kwa mzinda wa St. Petersburg. Pa 26 April 2016, khotili linamvetseranso kachiwiri mlanduwo ndipo woweruza anauimitsa kaye podikira kuti khoti lifufuzenso za Baibuloli. A Mboni za Yehova sanapatsidwe mwayi wofotokozapo mbali yawo ndipo khotilo linauza bungwe lina loona za maphunziro a chikhalidwe cha anthu kuti lifufuze za nkhaniyi. Koma umboni wabodza womwe bungweli linapereka m’mbuyomo, ndi womwe unachititsa kuti khotili litsegulire a Mboni mlandu wa Baibuloli. Zomwe khotili linachita polola kuti bungweli lifufuzenso za Baibulo la Dziko Latsopano, kunali kuphwanya lamulo lomwe Khoti lalikulu la ku Russia linaika. Khotilo linaika lamulo lakuti ngati munthu kapena bungwe linaperekapo kale umboni winawake m’khoti, munthu kapena bungwelo siliyenera kugwiritsidwanso ntchito pa nkhani yomweyo.

Dr. Gerhard Besier

Podikira zotsatira za bungwe lija, akatswiri ena akhala akufotokozapo maganizo awo pa nkhani ya Baibulo la Dziko Latsopano. Mmodzi wa akatswiriwa ndi Dr. Gerhard Besier yemwe ndi mtsogoleri wa bungwe lina loona za ufulu wa anthu komanso ulamuliro wa demokalase. Iye anati: “Akatswiri ambiri a Baibulo ochokera m’zipembedzo zosiyanasiyana padziko lonse lapansi, amanena kuti Baibulo la Dziko Latsopano, linamasuliridwa bwino kwambiri.

Bungwe lina lofufuza komanso kufalitsa nkhani la mumzinda wa Moscow, mwezi uliwonse limalemba komanso kutulutsa nkhani. Mu February 2016 bungweli linalemba nkhani yokhudza kugwiritsira ntchito molakwika lamulo la zinthu zoopsa. M’nkhaniyo analemba kuti: “Sitikuona choopsa chilichonse mu Baibulo la Dziko Latsopano.” Kuchokera mwezi umenewo, bungweli lakhala likutulutsa nkhani zotsutsa zomwe boma la Russia likuchita. Mwachitsanzo m’mwezi wa June 2016 linalemba kuti: “Tikufuna tibwerezenso kunena kuti, ‘Kumanga a Mboni za Yehova, kuletsa mabuku awo komanso kuwaletsa kuti asamachite misonkhano yawo ndi kuphwanya ufulu wawo wachipembedzo.’”

Yankhulani ndi:

International: David A. Semonian, Office of Public Information, 1-718-560-5000

Russia: Yaroslav Sivulskiy, 7-812-702-2691