Pitani ku nkhani yake

OCTOBER 14, 2015
RUSSIA

Akatswiri Ena Sanagwirizane ndi Zimene Dziko la Russia Lachita Poletsa JW.ORG

Akatswiri Ena Sanagwirizane ndi Zimene Dziko la Russia Lachita Poletsa JW.ORG

ST. PETERSBURG, ku Russia—Pa 21 July 2015, boma la Russia linaika lamulo loletsa webusaiti yovomerezeka ya Mboni za Yehova ya jw.org. Lamuloli linapangitsa kuti munthu aliyense amene angalimbikitse anthu kugwiritsa ntchito webusaitiyi aonedwe kuti akuphwanya malamulo a dzikoli. Dziko la Russia ndi loyamba kuletsa webusaiti ya jw.org.

Katswiri wina wazachipembedzo yemwenso ndi pulofesa pa yunivesite ina mumzinda wa Moscow, dzina lake Yekaterina Elbakyan, anati: “Ndikuona kuti webusaitiyi [jw.org] ndi yofunika chifukwa ili ndi mfundo zochokera kwa a Mboni za Yehova eniakewo zokhudza gulu lawo zomwe ndi zodalirika kusiyana ndi zimene anthu ena angalembe. . . . Sikuti a Mboni okha ndi amene amagwiritsa ntchito webusaitiyi. Anthu enanso amene amachita chidwi ndi zipembedzo zosiyanasiyana amaigwiritsanso ntchito. Apa ndikunena za akatswiri azachipembedzo ngati ineyo komanso za atolankhani ndi anthu ena amene amalemba zokhudza zipembedzo.”

“Ndikuona kuti webusaitiyi [jw.org] ndi yofunika chifukwa ili ndi mfundo zochokera kwa a Mboni za Yehova eniakewo.”—Yekaterina Elbakyan, yemwe ndi pulofesa pa yunivesite ina ku Moscow

Katswiri wina wazamalamulo okhudza ufulu wa anthu, dzina lake Lev Levinson, anati: “Masiku ano dziko la Russia lili ndi malamulo opatsa anthu ufulu wachipembedzo ndiponso onena kuti zipembedzo zonse ndi zololedwa ndi boma. Komabe boma la Russia layambanso kuchita zimene linkachita m’ma 1800. Layamba kuphwanya ufulu wa anthu wouza ena za chipembedzo chawo powalanda mabuku ndiponso poletsa mawebusaiti awo. Anthu amene akuchita zimenezi ndi oweruza ndiponso akatswiri omwe akugwiritsa ntchito malamulo molakwika uku akunena kuti akuletsa zinthu zoopsa zimene zingasokoneze anthu.”

Nkhaniyi inayamba mu 2013. Pa 7 August 2013, khoti lina ku Russia linazenga mlanduwu popanda kulola kuti anthu adzaonerere ndipo linagamula kuti webusaiti ya jw.org ndi “yoopsa.” Koma pa 22 January 2014, khoti lina linasintha zimene khoti loyambalo linagamula. Komabe wachiwiri kwa loya wa boma anachita apilo ku khoti lalikulu m’dziko la Russia. Pa 2 December 2014, khoti lalikululo linazenga mlanduwu koma a Mboni sanakhalepo chifukwa sanaitanidwe. Khotili linagamulanso kuti webusaiti ya a Mboni ndi “yoopsa” ngakhale kuti linavomera zoti pawebusaitiyi palibe mabuku omwe boma linaletsa. A Mboni anachita apilo kwa tcheyamani wa khoti lalikululi koma sizinatheke. Izi zinachititsa kuti pa 21 July, 2015, unduna wazachilungamo wa ku Russia ugamule kuti webusaitiyi ili m’gulu la zinthu zoopsa ndipo sikuloledwanso m’dziko lonse la Russia.

Yaroslav Sivulskiy, yemwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku Russia, anafotokoza zotsatirapo za kuletsedwa kwa webusaitiyi. Iye anati: “Tikudandaula kuti boma la Russia lachita zimenezi popanda zifukwa zomveka. Kuletsedwa kwa webusaiti yathuyi kwasokoneza kupembedza kwa anthu oposa 170,000 omwe ndi Mboni za Yehova m’dzikoli. Anthu pafupifupi 285,000 ku Russia ankalowa pawebusaitiyi tsiku lililonse. Izi zikusonyeza kuti ngakhale anthu amene si a Mboni atsekerezedwa mwayi woti aphunzire zinthu zothandiza za m’Baibulo.”

Mneneri wa Mboni za Yehova padziko lonse dzina lake J. R. Brown analankhulapo pa nkhaniyi kuchokera kulikulu lathu ku Brooklyn, New York. Iye anati: “Pawebusaiti yathu ya jw.org pali mavidiyo amene anthu amawakonda kwambiri, mabuku ofotokoza Baibulo m’zilankhulo zambiri ndiponso magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, omwe amafalitsidwa kwambiri kuposa magazini ena onse. Anthu akhala akugwiritsa ntchito webusaitiyi pa zionetsero zikuluzikulu za mabuku komanso kumasukulu ambiri. Yakhala ikuthandizanso anthu padziko lonse komanso inkagwiritsidwa ntchito ndi anthu ambiri ku Russia. Kunena zoona, webusaitiyi ndi yothandiza kwambiri.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Russia: Yaroslav Sivulskiy, tel. +7 812 702 2691