ST. PETERSBURG, Russia—Pa January 22, 2014, a Mboni za Yehova awina mlandu m’dziko la Russia pamene khoti lalikulu linasintha zimene khoti laling’ono linagamula zoti webusaiti ya jw.org itsekedwe m’dzikoli.

Khoti lalikulu la Tver linakana chigamulo chomwe chinaperekedwa pa August 7, 2013 ndi khoti laling’ono la Tsentralniy. Khoti lalikululi linanena kuti chigamulo cha khoti laling’ono choti webusaiti ya jw.org iletsedwe, chinali chopanda chilungamo, chifukwa a Mboni za Yehova, omwe ndi eni ake a webusaitiyi sanapatsidwe mwayi woti afotokoze mbali yawo pa mlanduwu. Woimira boma pa milandu ku Tver, anakasuma mlanduwu kukhoti, chifukwa chakuti webusaiti ya jw.org inali ndi mabuku omwe makhoti a m’dziko la Russia amati ndi “oopsa.” A Mboni za Yehova atauzidwa kuti khoti lagamula kuti mabuku awo ena ndi oopsa, nthawi yomweyo anatseka mbali zina pawebusaiti ya jw.org n’cholinga choti mabukuwo asamaoneke pawebusaitiyi m’dziko la Russia. Khoti lalikulu la Tver linatsimikizira kuti a Mboni ankatsatira zimene malamulo a dziko la Russia amanena ndipo khotili linasintha chigamulo chimene khoti laling’ono linapereka. A Mboni za Yehova akuyesetsabe kukambirana ndi makhoti a m’dziko la Russia pa nkhani yoti mabuku awo ena ndi “oopsa.” Ndipo a Mboniwa anapereka madandaulo awo ambiri ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya, n’cholinga choti makhoti a ku Russia asinthe malamulo oletsa mabuku awo ena.

Bambo Grigory Martynov, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku Russia anati: “Tikusangalala kuti oweruza mlanduwu anaona kuti webusaiti yathu ikuthandiza anthu komanso aona kuti tikuyesetsa kugwirizana ndi zimene makhoti akugamula pa nkhaniyi. Tipitirizabe kuyesetsa kumenyera nkhondo kuti mabuku athu asaletsedwe ndiponso kuti ufulu wa anthu a ku Russia woti azithandizidwa kwambiri ndi ntchito yathu yophunzitsa Baibulo upitirire.”

Bambo J.R. Brown omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova kulikulu lawo la padziko lonse, anati: “A Mboni za Yehova padziko lonse akusangalala chifukwa choti tawina mlanduwu. Popeza tawina mlanduwu, anthu onse a m’dziko la Russia apitiriza kugwiritsa ntchito webusaitiyi, yomwe ndi yothandiza kwambiri pophunzira Baibulo.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera ku Mayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Russia: Grigory Martynov, tel. +7 812 702 2691