Pitani ku nkhani yake

APRIL 20, 2017
RUSSIA

Khoti Lalikulu Kwambiri M’dziko la Russia Lagamula Kuti Likulu la Mboni za Yehova M’dzikolo Litsekedwe

NEW YORK—Pa milungu iwiri yapitayi, Khoti Lalikulu Kwambiri M’dziko la Russia lakhala likuzenga kuzenga mlandu wokhudza Mboni za Yehova kwa masiku 6. Lachinayi pa April 20, 2017, khotilo lagamula mogwirizana ndi zimene Unduna wa Zachilungamo m’dzikolo ukufuna, zoti Likulu la Mboni za Yehova m’dzikolo litsekedwe. Zimenezi zikutanthauza kuti mabungwe 395 omwe amaimira Mboni za Yehova m’dzikolo atsekedwanso. Zimene khotili lagamula zayamba kale kugwira ntchito.

A Yaroslav Sivulskiy omwe amalankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku Russia anena kuti: “Takhumudwa kwambiri ndi zimene khotili lachita ndipo tikuda nkhawa kwambiri ndi mmene chigamulochi chikhudzire ntchito yathu.” Iwo anafotokozanso kuti: “Tipanga apilo chigamulochi ndipo sitikukayika kuti posachedwapa tipatsidwanso ufulu wathu wolambira monga gulu lachipembedzo lokonda mtendere.”

A Mboni za Yehova ku Russia apatsidwa masiku 30 kuti apange apilo za nkhaniyi ndipo majaji atatu ndi amene adzawunikenso mlanduwu.

Lankhulani ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Russia: Yaroslav Sivulskiy, +7-911-087-8009