Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

APRIL 5, 2017
RUSSIA

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia Layamba Kuzenga Mlandu Waukulu Kwambiri Wokhudza Mboni za Yehova

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia Layamba Kuzenga Mlandu Waukulu Kwambiri Wokhudza Mboni za Yehova

NEW YORK—Lero Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia layamba kuzenga mlandu umene Unduna wa Zachilungamo ukufuna kuti Likulu la Mboni za Yehova m’dzikolo litsekedwe. Khotilo laimitsa kaye kuzenga mlanduwu ndipo lidzapitiriza pa Lachinayi, 6 April, 2017, nthawi ya 2:00 masana.

Pa 30 March, 2017, a Mboni analembera Khotili kalata n’cholinga chotsutsa zimene Unduna wa Zachilungamo unanenazi. Komabe, Khotili lakana zimene a Mboniwo ananena lisanaimitse kaye mlanduwu. Khotilo lakananso kuti akatswiri apereke umboni wosonyeza zimene zachititsa a Unduna wa Zachilungamo kuti anene kuti ntchito ya Mboni za Yehova iletsedwe. Komanso khotili lakana kuti anthu omwe anaona zinthu zosonyeza kuti umboni umene Unduna Wazachilungamo unapereka ndi wabodza wokhudza mipingo yosiyanasiyana ya Mboni za Yehova afotokoze zimene anaonazo.

Chifukwa chakuti mlanduwu ndi waukulu kwambiri, ofalitsa nkhani ambiri akulemba komanso kuulutsa mmene mlanduwu ukuyendera. Zina mwa nkhanizi ndi imene ili m’magazini yotchedwa Time yomwe inaikidwa pa intaneti pa 4 April ya mutu wakuti ‘Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia Likuona Ngati Kuli Koyenera Kuthetsa Chipembedzo cha Mboni za Yehova.’ Inanso ndi imene ili mu nyuzi pepala ya The New York Times yamutu wakuti ‘Akhristu Amene Amakhulupirira Kuti Kuchita Zachiwawa Komanso Kumenya Nkhondo N’kulakwa Aopsezedwa ndi Boma la Russia Kuti Ntchito Zawo Ziletsedwa Chifukwa Chochita Zinthu Zoopsa’ ya pa 5 April.

A David A. Semonian, omwe amayankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku likulu lawo lapadziko lonse ku New York ananena kuti: “Tikukhulupirira kuti Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia lilemekeza ufulu wa a Mboni anzathu woti azipemphera momasuka.” Iwo ananenanso kuti: “Anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse akutsatira mwachidwi mmene mlanduwu ukuyendera ndipo akufuna aone ngati boma la Russia liteteze a Mboni za Yehova, omwe ndi nzika zimene zimatsatira malamulo.”

Lankhulani ndi:

International: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Russia: Yaroslav Sivulskiy, +7-812-702-2691