NEW YORK—Lachitatu pa 19 April, 2017, anthu okwana 300 anasonkhana kudzamvetsera mlandu womwe Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia likuzenga pa nkhani imene a Unduna wa Zachilungamo ananena yoti Likulu la Mboni za Yehova m’dzikolo alitseke. Anthu ena anafika 2:00 m’mamawa kudzamvetsera nkhaniyi ndipo limeneli linali tsiku la 5 kuzenga mlanduwu. Zinthu zankhanza zimene akuluakulu a boma la Russia akhala akuchitira a Mboni kwa 10 zapitazi, zinafotokozedwa mwachidule pamene Khotilo linaunika zinthu zosiyanasiyana zokwana 43 zomwe zinaperekedwa kuti zigwiritsidwe ntchito pozenga mlanduwu.

Khotilo linaunika zinthu zosiyanasiyana zokwana 43 zomwe zinaperekedwa kuti zigwiritsidwe ntchito pozenga mlanduwu.

Pamene amaunika zikalatazo, maloya oimira Unduna wa Zachilungamo sanathe kunena chifukwa chomveka chokhudza malamulo chochititsa kuti Likulu la Mboni za Yehova litsekedwe. Sanathenso kupeza china chilichonse chosonyeza kuti Likulu la Mboni za Yehova kapena mabungwe oimira Mboni za Yehova amachita zinthu zoopsa. Mmodzi wa maloya oimira Likulu la Mboni za Yehova, a Yury Toporov, anauza Khotilo kuti pa zinthu zambiri zomwe zinaperekedwazo kuti zigwiritsidwe ntchito pozenga mlanduwo, panali mphoto komanso makalata oyamikira omwe boma linapereka ku Likulu la Mboni za Yehova chifukwa cha zinthu zabwino zomwe lakhala likuchita m’dzikolo kwa zaka zambiri. Panalinso umboni wosonyeza kuti mabungwe oimira Mboni za Yehova nawonso akhala akuchita zinthu zosiyanasiyana zomwe zathandiza kwambiri anthu m’madera osiyanasiyana. Kuonjezera pamenepo, zinthu zambiri zomwe zinaperekedwa pa mlanduwu zikusonyeza kuti kuyambira mu 2008, a Unduna wa Zachilungamo akhala akuchita chidwi ndi zimene mabungwe oimira Mboni za Yehova amachita koma sanapeze chilichonse chosonyeza kuti mabungwewa amachita zinthu zoopsa. Nawonso maloya oimira Unduna wa Zachilungamo anavomereza zimenezi.

Kutsogolo, kuchokera kumanzere kupita kumanja: a Anton Omelchenko, a Maksim Novakov, a Victor Zhenkov, komanso a Yury Toporov, omwe ndi maloya oimira Likulu la Mboni za Yehova ku Russia. Kumbuyo, kuchokera kumanzere kupita kumanja: a Vasiliy Kalin ndi a Sergey Cherepanov (chapansipansi), mamembala a komiti yoimira Likulu la Mboni za Yehova ku Russia.

Khotili likuyembekezeka kupitiriza mlanduwu pa 20 April , 2017, nthawi ya 2:00 masana.

Lankhulani ndi:

Kuchokera ku Mayiko Ena: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Russia: Yaroslav Sivulskiy, +7-911-087-8009