Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

JULY 2, 2013
RUSSIA

Khoti la ku Ulaya Lateteza Ufulu wa Mboni za Yehova pa Mlandu Wokhudza Kusungiridwa Chinsinsi

Khoti la ku Ulaya Lateteza Ufulu wa Mboni za Yehova pa Mlandu Wokhudza Kusungiridwa Chinsinsi

NEW YORK​—⁠Lachisanu pa June 6, 2013, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linalamula boma la Russia kuti lipereke chipukutamisozi kwa azimayi awiri, omwe ndi a V. Zhukova ndi a Y. Avilkina, cha ndalama zokwana madola 6,622 aliyense. Khotili linapereka chigamulochi chifukwa choti akuluakulu a boma la Russia anatenga zikalata zakuchipatala za azimayiwa, zomwe ndi zachinsinsi, popanda chilolezo. A khoti ananena kuti zimene boma la Russia linachitazi n’kuphwanya ufulu wofunika kwambiri wodzisungira chinsinsi, ndipo ufulu umenewu ndi wofunika “kulemekezedwa kwambiri” malinga ndi mfundo zimene mayiko a ku Ulaya anagwirizana pamsonkhano wawo.

Chigamulochi chaperekedwa patatha zaka 5 mlanduwu uli kukhoti. M’chaka cha 2007, mkulu woimira boma pa milandu mumzinda wa St. Petersburg analamula zipatala kuti zizimutumizira “zikalata zakuchipatala za munthu aliyense wa Mboni za Yehova amene wakana kuikidwa magazi kapena zigawo zamagazi,” popanda kufunsa kapena kupempha munthu wodwalayo. Zimenezi zinachititsa kuti pa March 9, 2009, a Mboni akasume ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya, pamlandu wakuti Boma la Russia Likulimbana ndi Avilkina Komanso Anthu Ena (Avilkina and Others v. Russia). M’chigamulo chake, khotilo linanena kuti zimene boma la Russia likuchitazo “n’zopondereza.” Khotilo linanenanso motsimikiza kuti panalibe “zifukwa zomveka” zimene zinachititsa kuti akuluakulu a bomawo aziona zikalata zachinsinsizi.

Polankhula mlanduwu utatha, bambo Grigory Martynov, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku Russia anati: “Zimene khoti lagamulazi zithandiza nzika zonse za ku Russia komanso anthu a m’mayiko onse amene ali m’Bungwe la Mayiko a ku Ulaya kuti anthu ena asamaphwanye ufulu wawo pa zinthu zofunika ngati zimenezi.”

Kuchokera m’mayiko ena:

Lankhulani ndi: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Russia: Grigory Martynov, tel. +7 812 702 2691