Pitani ku nkhani yake

APRIL 6, 2017
RUSSIA

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia Likupitiriza Kuzenga Mlandu Womwe Ukukhudza Mboni za Yehova

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia Likupitiriza Kuzenga Mlandu Womwe Ukukhudza Mboni za Yehova

Patsiku lachiwiri lozenga mlandu, Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia linapitiriza kuunika zimene Unduna wa Zachilungamo unanena zoti Likulu la Mboni za Yehova la m’dzikolo lithetsedwe. Mlanduwu unaimitsidwa kaye mpaka Lachisanu, pa April 7, 2017, nthawi ya 10:00 m’mawa.

A David A. Semonian, omwe amayankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku likulu lawo ku New York, anati: “Mmene mlanduwu wayendera lero, zasonyezeratu kuti a Unduna wa Zachilungamo alibe zifukwa zomveka pankhani imene akuneneza gulu lathu.” Iwo ananenanso kuti: “Koma taonanso kuti a Unduna wa Zachilungamo avomereza poyera kuti ngati ntchito ya Mboni za Yehova ingaletsedwe, a Mboniwo azizengedwa mlandu akapezeka atasonkhana pamodzi kuchita mapemphero awo. Tikukhulupirira kuti khotili ligamula nkhaniyi mwachilungamo ndipo sililola kuti ufulu wathu uphwanyidwe.”

Lankhulani ndi:

International: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Russia: Yaroslav Sivulskiy, +7-812-702-2691