Pitani ku nkhani yake

JULY 16, 2014
RUSSIA

Khoti la ku Russia Likuyembekezeka Kupereka Chigamulo: A Mboni za Yehova Akuimbidwa Mlandu Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

Khoti la ku Russia Likuyembekezeka Kupereka Chigamulo: A Mboni za Yehova Akuimbidwa Mlandu Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

Pa July 28, 2014, Khoti la mu mzinda wa Taganrog lipereka chigamulo pa mlandu womwe watha miyezi 15 wokhudza a Mboni za Yehova okwana 16. Akuluakulu a mumzinda wa Taganrog akuimba mlandu a Mboni za Yehova chifukwa chokonza komanso kupezeka pa misonkhano ya chipembedzo. Amboniwa akuimbidwanso mlandu chifukwa chouza ena zimene amakhulupirira ndipo imeneyi ndi ntchito imene a Mboni za Yehova onse padziko lonse amagwira. Ngati khotili ligamule kuti a Mboniwo ndi olakwa, ndiye kuti ziperekanso mphamvu ku makhoti ena m’dziko la Russia kuti aziimba mlandu wa Mboni za Yehova aliyense amene akusonkhana kapena kuuza ena zimene amakhulupirira.

Lankhulani ndi:

Kuchokera m’mayiko ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Russia: Grigory Martynov, tel. +7 812 702 2691