Pitani ku nkhani yake

21 JUNE, 2017
RUSSIA

Vidiyo Yosonyeza Apolisi ku Russia Akusokoneza Misonkhano ya Mboni za Yehova

Vidiyo Yosonyeza Apolisi ku Russia Akusokoneza Misonkhano ya Mboni za Yehova

NEW YORK—Vidiyo imene inatuluka posachedwapa ikusonyeza apolisi a ku Russia komanso apolisi a gulu lina loona za chitetezo (Federal Security Service) akusokoneza misonkhano imene a Mboni za Yehova ankachita mwamtendere pa 25 May, 2017, mu mzinda wa Oryol. Vidiyoyi inafalitsidwa pa webusaiti ya glavny.tv yomwe ndi ya bungwe lina lofalitsa nkhani m’dzikolo.

Pa 25 May, 2017 apolisi a dziko la Russia omwe anali ndi zida anasokoneza misonkhano imene a Mboni za Yehova ankachita mwamtendere mumzinda wa Oryol.

Vidiyoyi ikusonyeza a Dennis Christensen omwe ndi a ku Denmark akukambirana modekha ndi apolisiwo. Iwo anamangidwa patsiku lomweli ndipo mpaka pano akusungidwa m’ndende ngakhale kuti mlandu wawo sunazengedwe.

A Dennis Christensen, omwe kwawo ndi ku Denmark ndipo ndi mkulu mumpingo akukambirana ndi apolisi. Iwo anamangidwa ndi apolisi a gulu la FSB ndipo akhala ali m’ndende kuyambira pa 25 May, 2017.

A David A. Semonian omwe amalankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku likulu lawo lapadziko lonse ananena kuti: “Vidiyo imeneyi ndi umboni woonekeratu woti a Mboni za Yehova ndi anthu amtendere. Amachitabe zinthu mwamtendere ngakhale akuluakulu a boma awaopseze kapena kusokoneza misonkhano yawo. Zinthu zophwanya ufulu wachipembedzo ngati zimenezi zipitirirabe pokhapokha Khoti Lalikulu Kwambiri M’dziko la Russia lisinthe chigamulo chake chokhudza Mboni za Yehova. Tikudera nkhawa kwambiri m’bale wathu Dennis Christensen yemwe akumuletsa ngakhale kulankhula ndi mkazi wake pa foni kapena kuti amuone kundendeko. Tikukhulupirira kuti m’bale wathuyu atulutsidwa posachedwa m’ndende momwe akusungidwa ngakhale kuti sanalakwe chilichonse.”

Lankhulani ndi:

David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000