NEW YORK—Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia lamaliza kuzenga mlandu patsiku lachitatu, ndipo mlanduwu waimitsidwa kaye mpaka Lachitatu, pa 12 April, 2017, nthawi ya 10:00 m’mawa. Lero khotili linamvetsera umboni umene a Mboni za Yehova 4 anapereka. A Mboniwo anafotokoza mfundo zofunika kwambiri zotsutsa zimene a Unduna wa Zachilungamo ananena pankhani ya kutseka Likulu la Mboni za Yehova m’dzikolo komanso kuletsa ntchito yawo.

Woweruza milandu anafunsa a Unduna wa Zachilungamo mafunso ambiri n’cholinga choti afotokoze umboni wa zimene amaneneza a Mboni za Yehova zoti amachita zinthu zoopsa komanso kuti amagawira anthu mabuku oopsa. Undunawu sunapereke umboniwo. Poyankhula m’khotimo, a Vasiliy Kalin, omwe ali m’komiti yoimira Likulu la Mboni za Yehova ku Russia, ananena kuti: “Ndikufuna kukumbutsa a Unduna wa Zachilungamo kuti zimene akufuna zoti ntchito ya Mboni za Yehova iletsedwe zikhumudwitsa anthu amene amakufunirani moyo wosangalala komanso wamtendere.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera ku Mayiko Ena: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Russia: Yaroslav Sivulskiy, +7-911-087-8009