WARSAW, Poland—Pa January 27, 2015, anthu ambirimbiri adzasonkhana pa mwambo wokumbukira kuti patha zaka 70 kuchokera pamene anthu anatulutsidwa kundende ya Auschwitz. Ku ndendeyi ankazunzirako komanso kupherako anthu pa nthawi ya ulamuliro wa chipani cha Nazi ku Germany. Malowa anawakhazikitsa n’cholinga choti azipherako anthu a mitundu ina yomwe anthu a chipani cha Nazi ankadana nayo. Ankazunzirakonso a Mboni za Yehova a ku Germany konko komanso a m’mayiko ena.

Mwambowu ukukonzedwa ndi bungwe loona za zinthu zakale la Auschwitz-Birkenau State Museum ndiponso la International Auschwitz Council. Pamwambowu padzapezekanso a Bronisław Komorowski omwe ndi pulezidenti wa dziko la Poland ndiponso akuluakulu a boma ochokera m’mayiko osiyanasiyana. Mwambowu udzaulutsidwanso pa Intaneti.

Malo a Auschwitz ali mumzinda wa Oświęcim ku Poland, womwe unalandidwa ndi asilikali a chipani cha Nazi pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse. Poyamba inali ndende ya dziko la Germany ndipo inali ndi akaidi 700 a ku Poland omwe anafika kundendeyi mu June 1940. Posakhalitsa, malowa anakula kwambiri ndipo anali ndi ndende zoposa 40 komanso ndende zina ting’onoting’ono. Kundende ya Auschwitz-Birkenau kunali malo 4 opherako anthu powapopera mpweya wa poizoni ndipo anthu 20,000 ankaphedwa pa tsiku. Pa zaka 5 zimene ndendeyi inkagwira ntchito, anthu pafupifupi 1.1 miliyoni ndiponso a Mboni za Yehova oposa 400 anatumizidwa kundendeyi.

Webusaiti ya Auschwitz-Birkenau State Museum inanena kuti: “Mabuku ofotokoza za mbiri ya ndende ya Auschwitz, amangonena pang’ono zokhudza a Mboni za Yehova (kundendeko ankadziwika ndi dzina lakuti Ophunzira Baibulo) amene anamangidwa chifukwa chokana kusiya zimene ankakhulupirira. Anthuwa ndi oyeneradi kuwakumbukira chifukwa anayesetsa kutsatira zimene ankakhulupirira ngakhale kuti ankakhala mozunzika kundende.” Pali umboni wosonyeza kuti a Mboni anali gulu loyamba la akaidi otumizidwa kundendeyi ndipo a Mboni 35 pa 100 aliwonse anafera kundendeyi.

Bambo Andrzej Szalbot (Mkaidi–IBV 108703): Mu 1943, anamangidwa ndi asilikali a chipani cha Nazi pa mlandu wokana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira ndipo anatumizidwa kundende ya Auschwitz.

Chipani cha Nazi chinayamba kuzunza a Mboni mu 1933 ndipo kenako chinaletsa ntchito yawo m’dziko lonse la Germany. Mfundo zimene a Mboni ankatsatira zinkachititsa kuti asamatsatire zofuna za chipani cha Nazi. Mwachitsanzo, a Mboni ankakana kunena mawu akuti “Hitler ndi Mpulumutsi Wathu!,” chifukwa ankaona kuti Mulungu yekha ndiye woyenera kupatsidwa ulemu woterewu. A Mboniwo ankakananso kugwira nawo ntchito zonse zokhudzana ndi usilikali ndipo ankaonedwa kuti ndi oukira boma. Bambo Andrzej Szalbot, anatumizidwa kundende ya Auschwitz mu 1943 ali ndi zaka19. Iwo anena kuti: “Ukakana kulowa usilikali unkadziwiratu kuti ukupita kundende.” A Mboniwo anauzidwa kuti amasulidwa akangosaina chikalata chonena kuti asiya kukhala a Mboni ndiponso akanena kuti zimene a Mboni amaphunzitsa n’zabodza. Bambo Szalbot anakanitsitsa kusaina chikalatachi.

A Mboni ankauzidwa kuti amasulidwa akasaina chikalata ngati ichi chonena kuti asiya kukhala a Mboni.

Chipani cha Nazi chinkagwiritsa ntchito zilembo za “IBV” potchula a Mboni za Yehova. Zilembozi zinkaimira mawu a Chijeremani (Internationale Bibelforscher-Vereinigung) omwe ankatanthauza, Ophunzira Baibulo a Padziko Lonse ndipo limeneli linali dzina la gulu la Mboni za Yehova lovomerezeka ndi boma la Germany. Chipani cha Nazi chinakonzanso zoti a Mboni azisokerera kansalu kapepo pamayunifolomu awo. Kansaluka kanali ngati kachizindikiro komwe kankathandiza a Mboni kuti azidziwana mosavuta kundendeko. Iwo ankakumana madzulo aliwonse kuti azilimbikitsana oyang’anira ndendeyo asanabwere kudzawawerenga. A Mboniwo ankachitanso misonkhano yachinsinsi pofuna kuphunzira Baibulo ndi akaidi omwe ankachita chidwi ndi makhalidwe awo. Zimenezi zinachititsa kuti akaidi ambiri a kundende ya Auschwitz akhalenso a Mboni za Yehova.

Loweruka m’mawa pa January 27, 1945, asilikali a dziko la Soviet Union anafika ku Oświęcim. Mmene inkafika 3 madzulo a tsikuli, asilikaliwa anali atapulumutsa akaidi 7,000 m’ndende za Auschwitz I, Auschwitz II (Birkenau) ndiponso Auschwitz III (Monowitz).

Bambo Stanisław Zając. Anafika kundende ya Auschwitz pa February 16, 1943.

Asilikali a chipani cha Nazi ataona kuti asilikali a Soviet Union akuyandikira, anakakamiza akaidi ambiri a m’ndende zina za ku Auschwitz kuti atuluke ndipo pagululi panali bambo Stanisław Zając, omwe anali a Mboni za Yehova. Bambo Zając ndi akaidi ena pafupifupi 3,200 anakakamizidwa kutuluka m’ndende yaing’ono ya Jaworzno ndipo anawadutsitsa m’malo ozizira kwambiri omwe anali ndi madzi oundana. Asilikali a Nazi anachita dala zimenezi pofuna kuti akaidiwo afe. Zikuoneka kuti anthu osakwana 2,000 okha ndi amene anapulumuka pa anthu amene anayenda ulendo wa masiku atatu wopita kundende yaing’ono ya Blechhammer, yomwe inali kunkhalango. Bambo Zając ananena kuti pa nthawi imene iwowo ndi akaidi anzawo anabisala m’ndendeyi, ankamva phokoso la zida za nkhondo panja. Iwo anati: “Tinkamva akasinja akudutsa koma palibe amene analimba mtima kutuluka kuti aone komwe anachokera. Kutacha m’mawa tinaona kuti anali a dziko la Russia. . . . Kunabwera asilikali ambiri a ku Russia ndipo anatitulutsa m’ndendemo moti ukaidi wanga unathera pamenepo.”

Pa January 27 chaka chino, mwambo wokumbukira kuti patha zaka 70 kuchokera pamene anthu anatulutsidwa kundende ya Auschwitz, uchitikira m’mizinda yosiyanasiyana padziko lonse lapansi.

Lankhulani Ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Germany: Wolfram Slupina, tel. +49 6483 41 3110

Poland: Ryszard Jabłoński, tel. +48 608 555 097