Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

APRIL 29, 2014
NICARAGUA

Zivomerezi ku Nicaragua

Zivomerezi ku Nicaragua

Lolemba pa April 14, 2014, chivomerezi champhamvu kwambiri chinawononga zinthu kumpoto chakumadzulo m’tauni ya Managua, m’dziko la Nicaragua. Chivomerezichi chinali cha mphamvu zokwana 5.1 pa sikelo yoyezera mphamvu za zivomerezi. Chivomerezichi chinali chomaliza pa zivomerezi zotsatizana zimene zinachitika m’derali kwa masiku 4. Pa zivomerezizi, champhamvu kwambiri chinafika pa 6.6, pa sikelo yoyezera mphamvu za zivomerezi. Akuluakulu a ku ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Central America yomwe ili m’dziko la Mexico, anafotokoza kuti palibe munthu wa Mboni za Yehova amene anamwalira kapena kuvulala. Nyumba 7 za anthu a Mboni zinagweratu ndipo zina 21 zinawonongeka kwambiri. Nyumba ya Ufumu, yomwe ndi malo olambirira a Mboni za Yehova, ya m’tauni ya Nagarote inawonongeka kwambiri. Zimenezi zinachititsa kuti mipingo iwiri ya Mboni za Yehova yomwe inkasonkhana m’nyumbayo, isonkhane pamalo oimika magalimoto kuti ichite mwambo wapachaka wokumbukira imfa ya Yesu Khristu. Pa mwambowu panasonkhana anthu oposa 530, ndipo ena sanali a Mboni. Anthu a ku ofesi ya Mboni za Yehova akuthandiza a Mboni anzawo amene nyumba zawo zawonongedwa, powamangira nyumba zongoyembekera.

Lankhulani ndi:

Kuchokera ku Mayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Central America: Gamaliel Camarillo, tel. +52 555 133 3048