LILONGWE, Malawi—Pa 3 May 2017, ana awiri a Mboni za Yehova analoledwa kuyambiranso sukulu atawachotsa pa Khombe Primary School. Pa 13 February 2017, Aaron Mankhamba wazaka 18 komanso Hastings Mtambalika wazaka 15, anachotsedwa sukulu chifukwa chokana kuimba nawo nyimbo ya fuko. Anyamatawa anawalola kuyambiranso sukulu, makolo awo komanso oimira maofesi a Mboni za Yehova atakakumana ndi akuluakulu a pasukuluyo.

Pa nthawi imene amakambirana nkhaniyi, oimira maofesi a Mboni za Yehova, anaonetsa akuluakulu a sukuluyi makalata awiri ochokera ku boma la Malawi. Imodzi ya makalatawa inalembedwa mu 1997. Boma la Malawi linalembera a Mboni za Yehova kalatayi pofuna kuwauza kuti ndi ololedwa kuti asamaimbe nawo nyimbo ya fuko. Kalata ina inalembedwa mu 2017 ndipo boma la Malawi linalemba kalatayi pofuna kudziwitsa oyang’anira masukulu kuti azilemekeza ufulu wachipembedzo wa ana.

Hastings anafotokoza kuti anawalola kukayambiranso sukulu nthawi yolemba mayeso aboma itayandikira kwambiri. Hastings ananena kuti: “Tinali ndi nkhawa kuti sitikhalanso ndi mwayi wolemba nawo mayeso aboma ndipo mayesowa amabwera kamodzi pachaka.” Mwana wa sukulu akalephera mayesowa amafunikanso kubwereza kalasiyo.

A Augustine Semo ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku Malawi. A Semo anati: “Ana asukuluwa anasangalala kwambiri chifukwa chowalola kutsatira zimene amakhulupirira. Tikuthokoza akuluakulu asukuluyi polemekeza ufulu wachipembedzo wa anawa komanso kuwalola kuti ayambirenso sukulu.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera Kumayiko ena: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Malawi: Augustine Semo, +265-1-762-111