Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

4 JULY, 2017
KAZAKHSTAN

Boma la Kazakhstan Lalamula Kuti Ofesi ya Mboni za Yehova M’dzikolo Itsekedwe Kaye

Boma la Kazakhstan Lalamula Kuti Ofesi ya Mboni za Yehova M’dzikolo Itsekedwe Kaye

Pa 29 June, 2017, khoti lina ku Kazakhstan linagamula kuti ofesi ya Mboni za Yehova m’dzikolo itsekedwe kwa miyezi itatu komanso kuti ilipire ndalama pafupifupi 680,000 KZT ($2,107).

Khotili linagamula zimenezi apolisi apita kukayendera ofesiyi pa 17 May 2017. Anthu ambiri ankaonerera pomwe apolisi pafupifupi 40 omwe ananyamula zida komanso kuvala zophimba nkhope anabwera ku ofesiyo. A Mboni za Yehova akukonza zokadandaula kukhoti chifukwa cha zimene apolisiwa anachita.

Pa 5 June, 2017 apolisi anapita kukayendera ofesiyi ndipo ananena kuti panali zinthu zina zomwe anapeza kuti ndi zolakwika komanso zophwanya malamulo. A Mboni za Yehova anaona kuti zimene apolisiwo ankanena sizinali zoona komanso kuti poyendera malowo sanatsatire dongolo loyenera.

Zimene zikuchitika ku Kazakhstan zikufanana ndi zimene zikuchitikira a Mboni za Yehova ku Russia komwe akuopsezedwa ndi apolisi komanso kudedwa chifukwa cha zimene amakhulupirira. Panopo boma la Russia laletseratu ntchito ya Mboni za Yehova m’dzikolo. A Mboni za Yehova akufuna kupanga apilo pa chigamulo chimene boma la Russia linapereka pa 29 June ndipo aonetsetsa kuti achita apiloyo pofika pa 14 July, 2017.

Lankhulani ndi:

International: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Kazakhstan: Bekzat Smagulov, +7-747-671-45-01