Pitani ku nkhani yake

NOVEMBER 26, 2014
JAPAN

A Mboni za Yehova Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Kusefukira kwa Matope ku Hiroshima

A Mboni za Yehova Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Kusefukira kwa Matope ku Hiroshima

EBINA, Japan—Mvula yamphamvu yomwe inagwa m’mawa pa August 20, 2014 ku Hiroshima, inachititsa kuti matope asefukire n’kupha anthu 74 ndipo anthu 1,600 anasowa pokhala. Ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Japan inanena kuti palibe wa Mboni amene anafa kapena kuvulala, koma nyumba 8 za a Mboni zinawonongeka.

Mkati mwa nyumba yowonongeka ku Hiroshima.

Kwa maola atatu okha, kunagwa chimvula champhamvu chomwe chinawononga zinthu zambiri. Zimenezi zinachititsa kuti boma la dzikolo liyambitse ntchito yopulumutsa anthu. Ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Japan inakhazikitsa komiti yoti ithandize pa nthawi yovutayi komanso inapempha a Mboni ena kuti athandize pa ntchito yochotsa matope ndi zinyalala. Pogwira ntchitoyi, anthuwa ankaima pamzere n’kumapatsirana ndowa zamatope ndi zinyalala zomwe ankazichotsa m’nyumba za anthu. Anthuwo ankachotsa ndi kusunga katundu yemwe sanaonongeke ndi matopewo. Kenako ankathira mankhwala m’nyumbazo kuti aphe majelemusi.

A Mboni akuchotsa matope komanso zinthu zonyansa m’nyumba.

Nyuzipepala ya ku Japan yotchedwa Yomiuri Shimbun inalemba zimene wa Mboni za Yehova wina dzina lake Kayoko Nakamizo anachita pofuna kupulumutsa anthu ena. Nyuzipepalayi inanena kuti Kayoko, yemwe amakhala m’boma la Yagi m’dera la Asaminami Ward, anatuluka m’nyumba mwake n’kuyamba “kugogoda nyumba za anthu oyandikana nawo kuti aone ngati onse anali bwino.” Zimenezi zinathandiza kuti apulumutse munthu wina komanso anathandiza anthu ena kuti achoke malo a ngoziwo.

A Ichiki Matsunaga, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku Japan ananena kuti: “Tikumva chisoni ndi anthu amene akhudzidwa ndi kusefukira kwa matopewa. Ngakhale kuti ndi nthawi yovuta, tikupitiriza kudalira Yehova pamene tikuyesetsa kuthandiza komanso kulimbikitsa anthu a m’dera lathu.”

Mungalankhule ndi:

Kuchokera M’mayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000+1 718 560 

Japan: Ichiki Matsunaga, tel. +81 46 233 0005