Italy

MAY 23, 2018

Kufunsa a Luca P. Weltert, M.D.

“Taona kuti pali kusintha kwakukulu chifukwa chochepetsa kugwiritsa ntchito magazi pothandiza odwala ndipo zimenezi sizinakhudze odwala a Mboni okha, koma zakhudzanso dziko lonse lapansi chifukwa pali maumboni ochuluka osonyeza kuti kuchepetsa kugwiritsa ntchito magazi kuli ndi zotsatira zabwino kwambiri.”

MAY 23, 2018

Msonkhano Wofunika Kwambiri Wokambirana Zimene Zachitika pa Nkhani Yothandiza Odwala Popanda Kuwaika Magazi Unachitikira ku Yunivesite ya Padua

Anthu akhala akukhulupirira kuti kuika munthu magazi kulibe vuto lililonse ndipo ndi njira yokhayo yopulumutsira moyo wa anthu omwe adwala kwambiri kapena omwe akufunika kupangidwa opaleshoni. Koma anthu ambiri omwe anayankhula pamsonkhanowu, sanagwirizane ndi maganizo amenewa.