TEL AVIV—Kuyambira pa 26 November mpaka pa 2 December, 2017, anthu 1,700 anapita kumalo omwe a Mboni za Yehova ankaonetsera zinthu amene ali m’nyumba yoonetsera zinthu zakale ya Hatachana. Cholinga cha chionetserocho chinali choti anthu ambiri adziwe mavuto amene a Mboni za Yehova anakumana nawo pa nthawi ya ulamuliro wa chipani cha Nazi.

Zinthu zimene anthu ankaona kumalowa zinali monga vidiyo yosonyeza zomwe zinkachitika pa nthawiyo, zithunzi zosonyeza zinthu zakale, komanso yunifolomu yomwe a Mboni omwe anali m’ndende pa nthawiyo ankavala. Yunifolomuyi inasokedwa ndi wa Mboni wina yemwe anamangidwa nawo koma anapulumuka. Koma chinthu chosangalatsa kwambiri pachionetserocho chinali zithunzi 27 zomwe zinajambulidwa ndi a Johannes Steyer zosonyeza zomwe anakumana nawo pa nthawi imene anali m’ndende. Iwo anabadwa mu 1908 ndipo anamwalira mu 1998. Bambo Steyer, omwe anali a Mboni za Yehova, anazunzidwa ndi chipani cha Nazi kwa zaka 10, komanso anaikidwa m’ndende zoipa kwambiri monga za Buchenwald, Mauthausen, Sachsenburg, komanso Sachsenhausen. A Steyer anamaliza kujambula zithunzizo m’zaka za m’ma 1970 ndipo anajambula zithunzizo pokumbukira zithunzi zomwe anaziona ali m’ndende komanso zimene zinawachitikira pamene anali kundendeko.

Mlendo akuyang’ana yunifolomu yomwe anthu ankavala pa nthawi ya ulamuliro wa Nazi yomwe inasokedwa ndi wa Mboni wina yemwe anapulumuka ku nkhanza za ulamulirowu.

Pulofesa Emeritus Yair Auron

Pofotokoza za kufunika koonetsa anthu zinthu ngati zimenezi ku Tel Aviv, a Yair Auron, omwe ndi katswiri wa mbiri yakale komanso pulofesa yemwe anapuma pantchito pa yunivesite ina ku Isiraeli, anati: “Ndikuganiza kuti n’zofunika kwambiri kuti ana a sukulu makamaka amene ali ku sekondale abwere ku malo achionetserowa, chifukwatu n’zomvetsa chisoni kuti anthu amadziwa zinthu zochepa kwambiri zokhudza Mboni za Yehova. Anthu ambiri a ku Isiraeli sadziwa chilichonse chokhudza Mboni za Yehova komanso zimene anakumana nazo mu ulamuliro wa chipani cha Nazi.”

A Mauro Trapanese, omwe amayankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku Isiraeli, anati: “Cholinga cha chionetserochi sichinali kungophunzitsa anthu za mavuto amene a Mboni za Yehova anakumana nawo mu ulamuliro wa chipani cha Nazi, koma kufotokozeranso anthu chinthu chapadera chomwe chinachitika pa nthawiyo. Mwachitsanzo, tinazindikira kuti anthu ambiri omwe anabwera sankadziwa kuti a Mboni za Yehova anapatsidwa mwayi woti akhoza kutulutsidwa m’ndende ngati atachoka m’chipembedzo chawo, zomwe zinali zosiyana ndi anthu a zipembedzo zina. Kufotokoza mfundo zofunika kwambiri koma zimene anthu ambiri sazidziwa ngati zimenezi, kunathandiza kuti chionetserochi chiyende bwino kwambiri.”

Pulofesa Gideon Greif

Pulofesa Gideon Greif, katswiri wa mbiri yakale yemwe amadziwa kwambiri mbiri ya ku Auschwitz, ananena kuti: “A Mboni za Yehova anali m’gulu la anthu abwino omwe anazunzidwa ndiponso kuphedwa chifukwa chokhala okhulupirika ku zimene amakhulupirira komanso chikumbumtima chawo.”

Dr. Batya Brutin

Pofotokoza mwachidule ulendo wake wa ku chionetserochi, Dr. Batya Brutin, omwe ndi katswiri wa zithunzi zakale zosonyeza kuphedwa kwa anthu mu ulamuliro wa chipani cha Nazi, anati: “Ndikuganiza kuti kuphunzira zokhudza zimene a Mboni za Yehova anakumana nazo mu ulamuliro wa chipani cha Nazi, kukhoza kuthandiza anthu kukhala ndi makhalidwe abwino omwe angachititse kuti zinthu ziziyenda bwino m’dzikoli.”

Ngakhale kuti okonza chionetserochi anapanga malo oonetserapo zinthu ogwiritsa ntchito kamodzi kokha, nthumwi za m’masukulu ambiri zinapempha kuti pakhale malo ambiri oonetserapo zinthu zomwe zinachitikira a Mboni za Yehova.

Lankhulani ndi:

Kuchokera ku Mayiko Ena: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Ku Israel: Mauro Trapanese, +972-54-568-1912