Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

May 6, 2015
GUATEMALA

Sukulu za ku Guatemala Zikupempha Mabuku a Mboni za Yehova Pofuna Kuthetsa Nkhanza Zimene Achinyamata Akuchita

Sukulu za ku Guatemala Zikupempha Mabuku a Mboni za Yehova Pofuna Kuthetsa Nkhanza Zimene Achinyamata Akuchita

MEXICO CITY—Sukulu zitatu za ku Guatemala zinapempha mabuku kwa a Mboni za Yehova n’cholinga choti ana a sukulu azigwiritsa ntchito pophunzira. A Mboniwo anavomera ndipo anapereka mabuku 3,500 a chinenero cha Quiché komanso Chisipanishi. Chinenero cha Quiché chimalankhulidwa ndi amwenye a ku America amene amatchedwa Amaya. Anthuwa amakhala kumadera okwera a kumadzulo kwa dziko la Guatemala.

Sukulu Yapulaimale ya ku Paraje Xepec: Mphunzitsi akuphunzitsa pogwiritsa ntchito Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo lomwe a Mboni za Yehova anapereka.

Aphunzitsi a m’sukuluzi anapempha mabuku kwa a Mboniwa chifukwa iwowa ali m’gulu la mabungwe ochepa omwe amalemba mabuku m’chinenero cha Quiché. Aphunzitsiwa ananenanso kuti mabuku ambiri omwe a Mboniwa amalemba amakhala ndi nkhani zimene zingathandize achinyamata a ku Guatemala. M’kalata yawo yopempha mabukuwa, Pulofesa Maria Cortez ananena kuti anapempha mabukuwo n’cholinga choti “akathandize ana a sukulu kuti asataye chikhalidwe chimene anthu amafunika kukhala nacho.”

Sukulu ya Pulaimale ya Elisa Molina: Ana a sukulu akuwerenga Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo la chinenero cha Quiché.

Kafukufuku amene anachitika posachedwapa akusonyeza kuti achinyamata ambiri m’dzikoli amakonda kuchita zachiwawa. Zimenezi zachititsa kuti m’dzikoli mukhazikitsidwe mabungwe othandiza kuthetsa zachiwawa omwe amafotokozera “ana a sukulu, makolo, aphunzitsi, akuluakulu a boma komanso anthu ena zimene angachite kuti aliyense azikhala wotetezeka. Mabungwewa amakonzanso zochitika zosiyanasiyana zosangalatsa ndiponso amaphunzitsa achinyamata ndi achikulire omwe ntchito zosiyanasiyana zamanja.” Kuwonjezera pamenepa, aphunzitsi a sukulu ya INEBOA, sukulu ya Elisa Molina, komanso sukulu yapulayimale ya ku Paraje Xepec, anapempha mabuku akuti Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo a chinenero cha Quiché. Sukulu ya INEBOA inapemphanso mabuku akuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, buku loyamba ndi lachiwiri, a chinenero cha Chisipanishi. Kenako inapereka mabukuwa kwa makolo kuti azithandizira ana awo akamalemba homuweki pa phunziro lina la zachikhalidwe. Akuluakulu a sukuluyi anaikanso vidiyo ina ya Mboni za Yehova yamutu wakuti Mwana Wolowerera m’gulu la zinthu zoti ana aziphunzira pasukuluyi.

Bambo Erick De Paz, amene ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku Guatemala, anati: “Ngakhale kuti cholinga chathu chachikulu ndi kupita kunyumba za anthu kukawauza uthenga wa m’Baibulo, tikusangalala kuona kuti mabuku athu akuthandizanso aphunzitsi komanso makolo pophunzitsa achinyamata.”

Kuchokera M’mayiko ena:

Lankhulani ndi: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Guatemala: Juan Carlos Rodas, tel. +502 5967 6015

Mexico: Gamaliel Camarillo, tel. +52 555 133 3048