Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

NOVEMBER 4, 2014
GREECE

Zokhudza Misonkhano ya Mayiko: A Mboni za Yehova Anachita Msonkhano M’bwalo la Masewera la Olympic ku Greece

Zokhudza Misonkhano ya Mayiko: A Mboni za Yehova Anachita Msonkhano M’bwalo la Masewera la Olympic ku Greece

A Samuel Herd (kumanja) a m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova tsiku lililonse kumapeto kwa msonkhanowo, ankakamba nkhani yochokera m’Baibulo ndipo munthu wina ankamasulira m’Chigiriki.

Pa June 18, anthu 305 anabatizidwa pa msonkhanowu ku Greece ndipo ku Cyprus anabatizidwa anthu 32, onse anakwana 337.

ATHENS, Greece—Kuyambira pa June 27 mpaka 29, 2014, a Mboni za Yehova anachita msonkhano wa mutu wakuti “Pitirizani Kufunafuna Ufumu wa Mulungu Choyamba.” Msonkhanowu unachitikira m’bwalo la masewera la Olympic mumzinda wa Athens ku Greece komwe kunachitikira masewera a Olympic mu 2004. Anthu okwana 35,863 anachitira msonkhano kusitediyamuyi. Ku Belgium ndi ku Cyprus, anthu okwana 3,093 anamvetsera komanso kuonera nkhani zina za msonkhanowu pa telefoni ndi pa TV. Izi zinachititsa kuti chiwerengero cha anthu opezeka pa msonkhanowu chifike 38,956.

Pa msonkhanowu panafika anthu ambiri ochokera m’mayiko ena monga ku Croatia, Hungary, Korea, Romania, South Africa, Turkey ndi United States. A Christina Michail omwe amayang’anira sitediyamu ya Olympic anati: “Zinali zochititsa chidwi komanso zosangalatsa kuona anthu a mitundu yosiyanasiyana atakhala pamodzi, kujambulana komanso kuchita zinthu limodzi mwamtendere ndi mwachikondi . . . Nthawi zambiri, anthu amabwera pa malo ano kudzachita masewera osiyanasiyana koma sasonyeza makhalidwe abwino. N’chifukwa chake tasangalala komanso kuchita chidwi kwambiri ndi msonkhano umenewu.”

Anthu ali pa msonkhano m’bwalo la masewera la Olympic mumzinda wa Athens.

A Robert Kern, omwe amalankhula m’malo mwa ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Greece, anati: “Talandira makalata ochokera kwa anthu osiyanasiyana omwe akuyamikira msonkhano umenewu. Iwo akuyamikira kuti analimbikitsana komanso kusangalala ndi abale awo. Kunena zoona, zinali zosangalatsadi kusonkhana pamodzi ndi abale anthu a m’mayiko osiyanasiyana.”

Kuchokera M’mayiko Ena:

Lankhulani ndi: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Greece: Babis Andreopoulos, tel. +30 210 617 8606