Pitani ku nkhani yake

20 OCTOBER, 2015
GHANA

A Mboni za Yehova Anathandiza ku Ghana Kutasefukira Madzi

A Mboni za Yehova Anathandiza ku Ghana Kutasefukira Madzi

ACCRA, Ghana—Chakumapeto kwa mwezi wa August 2015, a Mboni za Yehova anamaliza ntchito yothandiza anthu amene anakhudzidwa ndi ngozi ya kusefukira kwa madzi, munzinda wa Accra ku Ghana. Ngoziyi inawononga katundu komanso inapha anthu oposa 200.

A Mboni za Yehova ku Ghana akuloza malo amene madzi anafika panyumba ya anzawo kutachitika ngozi ya kusefukira kwa madzi.

Pa ngoziyi palibe wa Mboni za Yehova amene anamwalira. Komabe a Mboni ena 250 ankasowa pokhala. Pa 4 June , 2015, ngoziyi itangochitika ngati dzulo lake, ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya ku Ghana inakhazikitsa komiti yoti ikathandize anthu. Komitiyi inapereka mabulangete, zovala komanso madzi. Inathandiza kukonza komanso kumanga nyumba zomwe zinawonongeka. A Mboni a munzinda wa Accra anathandizanso kwambiri chifukwa ankasunga a Mboni anzawo omwe analibe pokhala chifukwa cha ngoziyi.

Komiti yothandiza anthu amene anakhudzidwa ndi ngozi ya kusefukira kwa madzi, Dossou Amevor (kumanzere) akuyang’anira ntchito yogawa mabulangete pa Nyumba ya Ufumu ya Atiman m’dera la Madina ku Accra.

Madzi osefukirawo anawononga zinthu zina pamalo osungirapo mafuta a galimoto, moti anayambitsa moto woopsa womwe unawononga mapaipi amadzi m’dera la Adabraka. Zimenezi zinachititsa kuti madzi azisowa. Choncho ofesi ya nthambi inaika thanki ya madzi pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ya ku Adabraka ndipo a Mboni komanso anthu ena a m’deralo ankabwera kudzatunga madzi.

Loweruka pa 6 June, ofesi ya nthambi inatumiza madokotala atatu komanso manesi awiri a Mboni ku Alajo ndi Adabraka kuti akathandize a Mboni anzawo komanso anthu ena omwe anavulala pa ngoziyo. Madokotalawa anathandiza anthu amene ankadwala malungo, chifuwa komanso kutsegula m’mimba. A Mboni ochokera ku ofesi ya nthambi komanso m’deralo, anachezera a Mboni anzawo amene anakhudzidwa ndi ngoziyi kuti awalimbikitse.

Madokotala ndiponso manesi ali m’Nyumba ya Ufumu yomwe inkagwiritsidwa ntchito pothandiza anthu ovulala.

Yemwe amalankhula m’malo mwa a Mboni za Yehova ku Ghana, dzina lake Nathaniel Gbedemah anati: “Tili ndi chisoni kwambiri chifukwa cha anthu amene anamwalira pa ngoziyi komanso katundu amene anawonongeka. Ndiye monga mmene a Mboni za Yehova amachitira m’madera ena, nafenso tikufuna kuthandiza komanso kulimbikitsa anthu omwe akhudzidwa ndi ngoziyi.”

Lankhulani ndi:

Kumayiko ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Ghana: Nathaniel Gbedemah, tel. +233 30 701 0110